Pitani ku nkhani yake

Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?

Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?

Yankho la m’Baibulo

 Aramagedo ndi nkhondo yomaliza ya pakati pa maboma a anthu ndi Mulungu. Ngakhale panopa, maboma amenewa limodzi ndi otsatira awo amatsutsa Mulungu pokana kugonjera ulamuliro wake. (Salimo 2:2) Koma nkhondo ya Aramagedo idzathetsa ulamuliro uliwonse wa anthu.​—Danieli 2:​44.

 Mawu akuti “Aramagedo” amapezeka kamodzi kokha m’Baibulo, pa Chivumbulutso 16:16. Ulosi wa m’buku la Chivumbulutso umasonyeza kuti “mafumu a dziko lonse lapansi” adzasonkhanitsidwa “pamodzi kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Aramagedo,” “kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”​—Chivumbulutso 16:14.

 Ndi ndani amene adzamenye nkhondo ya Aramagedo? Yesu Khristu adzatsogolera gulu lankhondo la kumwamba pokagonjetsa adani a Mulungu. (Chivumbulutso 19:11-16, 19-21) Adani amenewa ndi amene amatsutsa ulamuliro wa Mulungu komanso amene salemekeza Mulunguyo.​—Ezekieli 39:7.

 Kodi nkhondo ya Aramagedo idzachitika kumayiko a ku Middle East okha? Ayi. Nkhondo ya Aramagedo sidzamenyedwa m’dera limodzi padziko lapansili. M’malomwake, nkhondoyi idzachitika padziko lonse lapansi.​—Yeremiya 25:32-34; Ezekieli 39:17-20.

 Mawu akuti Aramagedo, omwe nthawi zina amalembedwa kuti “Haramagedo” (m’Chiheberi Har Meghiddohnʹ), amatanthauza “Phiri la Megido.” Pa nthawi ina kale kwambiri, Megido unali mzinda ku Isiraeli. Mbiri yakale imasonyeza kuti nkhondo zoopsa kwambiri zinkachitikira m’dera limenelo. Ndipo nkhondo zina zimene zinachitika m’derali zinatchulidwa m’Baibulo. (Oweruza 5:19, 20; 2 Mafumu 9:27; 23:29) Komabe, mawu akuti Aramagedo sangatanthauze malo enieni a pafupi ndi mzinda wakale wa Megido. Kudera limenelo kulibe phiri lalikulu lomwe adani onse a Mulungu angakwanepo, ngakhale titaphatikiza malo onse a m’chigwa cha Yezereeli. M’malomwake, mawu akuti Aramagedo akutanthauza zimene zidzachitike padziko lonse, anthu a mitundu yonse akadzasonkhana pofuna kulimbana komaliza ndi ulamuliro wa Mulungu.

 Kodi chidzachitike n’chiyani pa nkhondo ya Aramagedo? Ngakhale kuti sitikudziwa kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake powononga adani ake, tikudziwa kuti ali ndi zida zimene anazigwiritsapo ntchito m’mbuyomo, monga matalala, zivomerezi, mvula yoopsa, moto ndi sulufule, mphenzi, komanso miliri. (Yobu 38:22, 23; Ezekieli 38:19, 22; Habakuku 3:10, 11; Zekariya 14:12) Tikudziwanso zoti adani ena a Mulungu adzaphana okhaokha chifukwa chosokonezeka koma pamapeto pake adzadziwa kuti Mulungu ndi amene akuchititsa zimenezo.​—Ezekieli 38:21, 23; Zekariya 14:13.

 Kodi dziko lidzatha pa Aramagedo? Sikuti Aramagedo idzawononga kapena kuthetsa dziko lapansili ayi. Zili choncho chifukwa Mulungu analenga dzikoli n’cholinga choti anthu azikhalamo mpaka kalekale. (Salimo 37:29; 96:10; Mlaliki 1:4) Ndipotu nkhondo ya Aramagedo sikuti idzawononga anthu onse, koma idzathandiza kuti anthu ena apulumuke. Baibulo limasonyeza kuti “khamu lalikulu” la atumiki a Mulungu lidzapulumuka.​—Chivumbulutso 7:9, 14; Salimo 37:34.

 Ngakhale kuti nthawi zambiri m’Baibulo mawu kuti “dziko” amatanthauza dziko lapansi lenilenili, nthawi zina mawuwa amatanthauzanso anthu ochita zoipa omwe samvera Mulungu. (1 Yohane 2:15-17) Choncho, tinganene kuti nkhondo ya Aramagedo idzachititsa “kutha kwa dziko lino lapansi,” kutanthauza anthu ochita zoipa.​—Mateyu 24:3, Chipangano Chatsopano Cholembedwa M’Chicheŵa Chamakono.

 Kodi Aramagedo idzachitika liti? Pofotokoza za “chisautso chachikulu” chimene chidzafike pachimake pa nkhondo ya Aramagedo, Yesu anati: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:21, 36) Ngakhale zili choncho, Baibulo limasonyeza kuti nkhondo ya Aramagedo idzachitika pa nthawi imene Yesu adzakhale pampando wachifumu koma mosaonekera kwa anthu. Nthawi imeneyi inayamba mu 1914.​—Mateyu 24:37-39.