Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amakana Mwaulemu Kuchita Nawo Miyambo Yosonyeza Kukonda Dziko Lawo?

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amakana Mwaulemu Kuchita Nawo Miyambo Yosonyeza Kukonda Dziko Lawo?

 A Mboni za Yehova amalemekeza maboma komanso zizindikiro zoimira dziko lawo. Timalemekeza zimene anthu ena amachita posonyeza kuti amakonda dziko lawo monga kulumbira, kuchitira sawatcha kapena kugwadira mbendera kapenanso kuimba nyimbo ya fuko lawo.

 Komabe, a Mbonife timasankha kusachita nawo miyambo imeneyi chifukwa timakhulupirira kuti ndi yosemphana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Choncho, nafenso timayamikira anthu ena akamalemekeza zomwe timasankha kukhulupirira.

Zimene zili munkhaniyi

 Kodi timatsatira mfundo za m’Baibulo ziti?

 Timatsatira mfundo za m’Baibulo ziwiri izi:

  •   Mulungu yekha ndiye woyenera kumulambira. Baibulo limanena kuti: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.” (Luka 4:8) Nthawi zambiri malumbiro kapenanso nyimbo za fuko zimakhala ndi mawu osonyeza kuti munthu walonjeza kuti azikonda kwambiri dziko lake kuposa china chilichonse. Choncho, a Mboni za Yehova amaona kuti n’kulakwa kuchita nawo miyambo yotereyi.

     A Mboni za Yehova amaonanso kuti kuchitira sawatcha mbendera kuli ngati kulambira mafano, ndipo Baibulo limaletsa kuchita zimenezi. (1 Akorinto 10:14) Olemba mbiri ena akuvomereza kuti mbendera za mayiko zimangofanana ndi zizindikiro za zipembedzo. Mwachitsanzo, a Carlton J. H. Hayes a analemba kuti: “Kukonda dziko lanu kuli ngati chipembedzo ndipo chizindikiro chachikulu chomwe anthu amalambira m’chipembedzochi ndi mbendera.” Ponena za Akhristu oyambirira, wolemba mbiri wina dzina lake Daniel P. Mannix, ananena kuti: “Akhristu ankakana . . . kupereka nsembe ku mizimu ya olamulira [a ku Roma]. Masiku ano zimenezi zingafanane ndi kukana kuchitira sawatcha mbendera.” b

    Ngakhale kuti a Mboni za Yehova sachitira sawatcha mbendera, iwo sawononga, kuwotcha kapena kuchita china chilichonse chosonyeza kusalemekeza mbendera kapena zizindikiro zina zam’dziko lawo.

  •   Mulungu amaona kuti anthu onse ndi ofanana. (Machitidwe 10:34, 35) Baibulo limanena kuti “kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu.” (Machitidwe 17:26) Pa chifukwa chimenechi, a Mboni za Yehova amaona kuti ndi kulakwa kuona kuti gulu linalake la anthu kapena mtundu winawake ndi wapamwamba kuposa ena. Iwo amalemekeza anthu amitundu yonse posatengera kuti anachokera kuti.​—1 Petulo 2:17.

 Tingatani ngati boma linakhazikitsa lamulo loti tizichita nawo miyamboyi?

 A Mboni za Yehova si otsutsa boma. Timakhulupirira kuti maboma omwe alipowa ndi “dongosolo la Mulungu” lomwe walilola kuti likhalepo. (Aroma 13:1-7) Timakhulupiriranso kuti Akhristu ayenera kumvera olamulira.​—Luka 20:25.

 Kodi a Mboni za Yehova amatani ngati olamulira akuwauza kuti achite zinthu zimene Mulungu amawaletsa? Nthawi zina zimatheka kupempha boma kuti lisinthe malamulo enaake. c Ngati boma lakana kusintha, a Mboni za Yehova amachita zinthu mwaulemu posankha “kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”​—Machitidwe 5:29.

 Kodi a Mboni za Yehova amakhala mbali ya mabungwe kapena magulu enaake a ndale?

 Ayi. A Mboni za Yehova salowerera nkhani za mabungwe omenyera ufulu kapena nkhani za ndale. Timakana kuchita nawo miyambo monga kulumbira, kuchitira sawatcha mbendera komanso kuimba nyimbo ya fuko chifukwa timatsatira mfundo za m’Baibulo zomwe timakhulupirira osati chifukwa ndife omenyera ufulu wa anthu.