Pitani ku nkhani yake

Kuchita Ulaliki wa Mashelefu Amatayala M’malo Amene Anthu Amakachitira Holide ku Germany

Kuchita Ulaliki wa Mashelefu Amatayala M’malo Amene Anthu Amakachitira Holide ku Germany

Masiku ano, anthu akamayenda m’matauni akuluakulu azolowera kumaona timashelefu tamatayala tokhala ndi mabuku ofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova. Mwachitsanzo, ku Germany, a Mboni ali ndi malo oimikamo timashelefuti m’matauni akuluakulu angapo monga ku Berlin, Cologne, Hamburg, Munich, ndi matauni ena.

Ndiyeno kodi anthu akakhala pa holide n’kupita m’matauni ang’onoang’ono amakapezanso timashelefuti? Kodi anthu omwe amakhala m’madera a m’mbali mwa nyanja kumpoto kwa dziko la Germany komanso omwe ali m’zilumba za Baltic ndi North seas akanasangalala ndi ulaliki wa timashelefuti? Zimene ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Central Europe inachita zinayankha mafunso amenewa. Iwo anakonza zoti kuyambira m’mwezi wa May mpaka October 2016, a Mboni pafupifupi 800 akalalikire kumadera akutali pogwiritsa ntchito timashelefu. Ena mwa a Mboniwo anachokera ku Vienna m’dziko la Austria ndipo mashelefuwo anaikidwa m’malo pafupifupi 60 a kumpoto kwa dziko la Germany.

“Mbali ya Tawuni”

A Mboni analandiridwa ndi manja awiri. Mayi wina wa Mboni amene anadzipereka kugwira nawo ntchitoyi anati: “Anthu anasonyeza chidwi. Anali ochezeka ndipo anali ndi mafunso ambiri komanso ankafuna kuti tizikambirana nawo.” Mayi winanso wa Mboni dzina lake Heidi wochokera ku Plön, anati: “Patadutsa masiku ochepa, anthu anayamba kutiona ngati anthu a mtauniyo. Enanso amene anatizindikira ankati akangotiona amatikwezera manja n’kumatibayibitsa.” Munthu wina yemwe ali ndi vuto losamva anayankhula m’chinenero chamanja kuti: “Muli paliponse!” Iye ndi anzake ena amachokera kumsonkhano wa anthu a vuto losamva chakummwera kwa dziko la Germany ndipo anakumananso ndi a Mboni ena kumeneko.

Anthu enanso a m’derali anathandiza kwambiri. Pa chilumba cha Wangerooge, mkulu wa apolisi wina anauza a Mboni zimene angachite kuti alalikire kwa anthu ambiri. M’dera la Waren an der Müritz, woyendetsa boti loonera malo anasonyeza anthu omwe anakwera m’botilo malo ena ochititsa chidwi. Ndipo anawasonyeza kashelefu kamateyala komwe kanali mphepete mwanyanja n’kuwauza kuti: “Apopo mutha kukaphunzira zokhudza Mulungu.” Anthu ambiri omwe anali patchuti anapita pomwe panali timashelefuti n’kumawerenga zomwe zalembedwa mumapositala a m’timashelefuti.

Anthu omwe anabwera kudzaona malo komanso a m’derali anachita chidwi kwambiri ndi timabuku titatu iti:

  • Kodi Mulungu Amatisamaliradi? Mayi wina amene anabwera kudzaona malo anati: “Ndakhala ndikudzifunsa funso limeneli kwa nthawi yaitali. Ndiye popeza kuti ndili pa tchuti, ndiwerenga kabukuka kuti ndipeze yankho lake.”

  • Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu. Bambo wina wachikulire anauza a Mboni kuti chipembedzo chinamukhumudwitsa. Ndiye a Mboniwo anamuthandiza kumvetsa kuti palibe munthu amene angathetse mavuto athu koma Mulungu yekha ndi amene angachite zimenezi. Munthuyo analandira kabuku ndipo analonjeza kuti akakawerenga.

  • Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo. Kabukuka kanakonzedwera ana, ndipo bambo wina analola kuti mwana wake wamkazi atenge kabukuka. Bamboyu anatenganso Buku Langa la Nkhani za M’Baibulo ndipo anati: “Buku limeneli likathandiza banja langa.”

Anthu ongodutsa anatenga mabuku opitirira 3,600. Ndipo anthu ena anapempha a Mboniwo kuti aziwayendera n’cholinga choti apitirize kukambirana nawo.

A Mboni omwe anagwira nawo ntchitoyi anasangalala kwambiri. A Jörg ndi akazi awo a Marina anapita ku dera lina lakufupi ndi Nyanja ya Baltic. Iwo ananena kuti: “Kugwira nawo ntchitoyi inali mphatso yapadera. Tinasangalala ndi chilengedwe cha Mulungu komanso kuti tinatha kukambirana ndi anthu zokhudza Mulungu.” Lukas, wa zaka 17 ananena kuti: “Ntchitoyi ndinaikonda kwambiri. N’zoona kuti ndinasangalala ndi zinthu zina koma chimene chinandisangalatsa kwambiri ndi kuuzako ena uthenga wa m’Baibulo, womwe ndi wamtengo wapatali.”