Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Mmene Mungathandizire Ana Anu kuti Asasokonezeke Ndi Nkhani Zoopsa

Mmene Mungathandizire Ana Anu kuti Asasokonezeke Ndi Nkhani Zoopsa

 Masiku ano nkhani zoopsa zikumapezeka paliponse. Mwachitsanzo, zikumaonetsedwa pa TV, zikumapezeka pafoni, pamatabuleti komanso pakompyuta.

 Nawonso ana amaonera nkhani zimenezi.

 Ndiye kodi mungathandize bwanji ana anu kuti asasokonezeke ndi nkhani zimenezi?

 Kodi nkhani zimenezi zimakhudza bwanji ana?

  •   Ana ambiri amakhudzidwa kwambiri ndi nkhani zimene amva kapena kuonera. Komabe, pali ana ena amene sasonyeza mmene zawakhudzira. a Anawa angasokonezeke kwambiri akaona kuti makolo awo akumakhala ndi nkhawa kwambiri chifukwa cha nkhanizi.

  •   Ana angamaganize zolakwika zokhudza nkhani zimene aonera. Mwachitsanzo, ena amaganiza kuti zimene aonazo zichitikira banja lawo. Komanso ana aang’ono omwe aonera vidiyo inayake yoopsa mobwerezabwereza, angayambe kumaganiza kuti zinthuzo zikungochitika mobwerezabwereza.

  •   Ana ena sangadziwe kuti nthawi zina olemba nkhani amakokomeza. Iwo sangadziwe kuti makampani ofalitsa nkhani amapeza phindu lalikulu ngati anthu ambiri akuonera nkhani zawo. Choncho, akhoza kukokomeza nkhanizo n’cholinga choti akope anthu ambiri.

 Kodi mungathandize bwanji ana anu ngati ayamba kuda nkhawa ndi nkhani zimene aonera?

  •   Muzionetsetsa kuti ana anu sakuonera kwambiri nkhani zoopsa. Zimenezi sizikutanthauza kuti ana anu asamadziwe zomwe zikuchitika padzikoli. Choncho, muziteteza ana anu kuti asapitirize kuwonera kapena kumvetsera nkhani zoopsa zomwe zikuonetsedwa mobwerezabwereza chifukwa sizingawathandize.

     “Nthawi zina ine ndi mwamuna wanga timakambirana zokhudza nkhani inayake yomwe yachitika osaganizira kuti zikhudza bwanji ana anthu omwe akutimvetsera.”—Maria.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa.”—Miyambo 12:25.

  •   Muziwamvetsera modekha komanso muziwayankha mogwirizana ndi msinkhu wawo. Ngati mwana wanu akuvutika kufotokoza zinthu zoopsa zimene zachitika, mungamuuze kuti ajambule zimene akufuna kunenazo. Ngati pali zinthu zimene zikumudetsa nkhawa, muzimufotokozera m’njira yoti amvetse. Komabe, muyenera kupewa kukambirana naye zinthu zimene sakufunikira kudziwa.

     “Mwana wathu amayamba kumva bwino tikamuuza kuti atifotokozere zimene zachitika, n’kumamumvetsera. Ndimaona kuti sizimathandiza tikamuuza kuti, ‘Ndi mmene zinthu ziliri masiku ano, tikungofunika kuzizolowera basi.’”—Sarahi.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.”—Yakobo 1:19.

  •   Muzithandiza mwana wanu kukhala ndi maganizo oyenera. Mwachitsanzo, lipoti lonena za anthu omwe agwidwa ndi zigawenga lingachititse kuti anthu ayambe kuganiza kuti zomwe aonazo zikhoza kuchitika. Choncho muzifotokozera ana anu zinthu zimene mwachita kuti iwo akhale otetezeka, komanso muzikumbukira kuti nkhani zoopsa zimaulutsidwa pa TV kapena pa wailesi chifukwa choti sizimachitikachitika osati chifukwa choti ndi zofala.

     “Muzithandiza ana anu kuona zinthu moyenera. Nthawi zambiri anthu amakhudzidwa ndi nkhani zimene aonera akaziganizira kwambiri.Choncho muzithandiza ana anu kuti aziganizira zinthu zabwino ndipo zimenezi zingawathandize kuti azisangalala.”—Lourdes.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Mtima wa munthu wanzeru umamuchititsa kuti asonyeze kuzindikira ndi pakamwa pake, ndipo umachititsa milomo yake kutulutsa mawu okopa.”—Miyambo 16:23.

a Ana aang’ono akakhala ndi nkhawa kwambiri amakodza pogona, amaopa kupita kusukulu komanso safuna kusiyana ndi makolo awo.