Pitani ku nkhani yake

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO—MARIYA MMAGADALA

“Ambuye Ndawaona Ine.”

“Ambuye Ndawaona Ine.”

Mariya Mmagadala akuyang’ana kumwamba, ndipo akupukuta misozi m’maso mwake. Ambuye omwe amawakonda apachikidwa pamtengo wozunzikirapo. Inali nyengo yozizira ndipo nthawi inali cha m’ma 12 koloko masana, “koma kunagwa mdima padziko lonse lapansi.” (Luka 23:44, 45) Kenako akukokera chovala chake m’mapewa n’kukakhala ndi azimayi omwe ali naye pafupi. Kadamsana yemwe amatenga maminitsi ochepa sakanachititsa kuti kukhale mdima wa maola atatuwu. Ndipo n’kutheka kuti Mariya ndi anthu ena omwe anaimirira pafupi ndi Yesu, anayamba kumva kulira kwa nyama zomwe zimamveka usiku okha osati masana. Anthu ena omwe analipo pa nthawiyo “anachita mantha kwambiri ndipo anati: ‘Ndithudi, uyu analidi Mwana wa Mulungu.’” (Mateyu 27:54) Ophunzira a Yesu ndi anthu ena, mwina ankaona kuti zimene zinkachitikazo ndi chizindikiro chakuti Yehova wakwiya chifukwa choti mwana wake wachitiridwa zinthu zankhanza.

Sizinali zophweka kwa Mariya Mmagadala kumuona Yesu akumva ululu, koma sankafuna kuchokapo. (Yohane 19:25, 26) N’zosakayikitsa kuti Yesu ankamva ululu woopsa. Nawonso mayi ake a Yesu ankafunika kuwatonthoza komanso kuwalimbikitsa.

Mariya ankafunitsitsa kuchita zonse zimene akanatha pothandiza Yesu, akakumbukira zimene Yesuyo anamuchitira. Poyamba anali mzimayi womvetsa chisoni ndiponso anthu sankamulemekeza. Koma Yesu anamuthandiza kwambiri moti anayamba kuona kuti moyo wake ndi wofunika komanso kuti uli ndi cholinga. Mariya anakhala mayi wa chikhulupiriro cholimba. N’chifukwa chiyani tikutero? Nanga tingaphunzire chiyani pa chikhulupiriro chimene anasonyeza?

Ankatumikira “Pogwiritsa Ntchito Chuma Chawo”

M’Baibulo, nkhani ya Mariya Mmagadala imayamba ndi kufotokoza za mphatso imene analandira. Yesu anamuthandiza kukhala ndi ufulu pomuchotsera ziwanda zimene zinkamuvutitsa. Nthawi imeneyo, sizinali zachilendo kumva kuti ziwanda zikuvutitsa anthu ambiri ndipo zinkathanso kulowa mwa anthu ena n’kumawalamulira. Sitikudziwa kuti ziwanda zinkamuvutitsa bwanji Mariya Mmagadala, koma chomwe tikudziwa n’chakuti anali ndi ziwanda zokwana 7. Chosangalatsa n’choti Yesu Khristu anamutulutsa ziwanda zonsezo.—Luka 8:2.

Zinthu zinayamba kumuyendera bwino kwambiri Mariya ndipo moyo wake unasintha. Pofuna kusonyeza kuyamikira zimene anamuchitira, anakhala wotsatira wokhulupirika wa Yesu. Komanso anachitapo kanthu ataona kuti Yesu komanso ophunzira ake akufunikira thandizo. Iwo ankafunikira chakudya, zovala komanso malo ogona. Popeza kuti amunawa anali osauka komanso sankagwira ntchito iliyonse, ankafunika kuwathandiza n’cholinga choti akwanitse kugwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa.

Ndiyeno Mariya ndi akazi ena anathandiza amunawa powapatsa zomwe ankafunikira. Akaziwa anatumikira Yesu ndi atumwi ake “pogwiritsa ntchito chuma chawo.” (Luka 8:1, 3) N’kutheka kuti ena mwa akaziwa anali olemera. Baibulo silisonyeza kuti akaziwa anathandiza anthuwo powakonzera chakudya, kuwachapira zovala kapena kuwapezera malo oti agone, akamachoka mudzi wina kupita mudzi wina. Koma limasonyeza kuti anali ofunitsitsa kuthandiza gulu la anthu omwe ankayenda ndi Yesu, omwe analipo pafupifupi 20. Zimene akaziwa ankachita zinathandiza kuti Yesu ndi ophunzira ake adzipereke pogwira ntchito yolalikira. N’zoona kuti Mariya sakanakwanitsa kubwezera Yesu zabwino zimene anamuchitira, komabe anasangalala kuona kuti wachita zonse zomwe akanatha.

Anthu ambiri masiku ano amaona kuti ndi apamwamba kuposa anthu omwe amagwira ntchito zooneka ngati zonyozeka pothandiza ena. Koma si mmene Mulungu amaonera zinthu. Mwachitsanzo, iye anasangalala kwambiri ataona kuti Mariya akudzipereka ndi mtima wonse pothandiza Yesu ndi ophunzira ake. Masiku anonso, pali Akhristu ambiri okhulupirika omwe amasangalala kugwira ntchito zooneka ngati zonyozeka pothandiza ena. Ndipotu nthawi zina kungochita zinthu zinazake zabwino kapena kulankhula mawu enaake abwino kwa munthu, kukhoza kukhala kothandiza kwambiri. Tikamachita zimenezi Yehova amasangalala.—Miyambo 19:17; Aheberi 13:16.

“Chapafupi ndi Mtengo Wozunzikirapo wa Yesu”

Mariya Mmagadala anali mmodzi mwa akazi ambiri omwe anatsatira Yesu popita ku Yerusalemu kukachita mwambo wa Pasika mu 33 C.E. (Mateyu 27:55, 56) Iye anakhumudwa kwambiri atamva kuti Yesu wamangidwa ndipo akumuzenga mlandu usiku. Ndipo zinthu zinafika poipa kwambiri. Bwanamkubwa Pontiyo Pilato, anakakamizidwa ndi atsogoleri a chipembedzo Chachiyuda komanso gulu la anthu, kuti apereke chigamulo choti Yesu aphedwe mochita kupachikidwa pamtengo. N’kutheka kuti Mariya ankaona Ambuye m’maganizo mwake, ali magazi okhaokha, akuvutika kuyenda mumsewu, atatoperatu ndi kunyamula mtengo wautali wozunzikirapo.—Yohane 19:6, 12, 15-17.

Pambuyo poti Yesu waphedwa komanso mdima womwe unagwa watha, Mariya Mmagadala ndi amayi ena anaima “chapafupi ndi mtengo wozunzikirapo wa Yesu.” (Yohane 19:25) Mariya anaona zonse zomwe zinkamuchitikira Yesu ndipo anamumva akuuza mtumwi Yohane kuti azikasamalira mayi ake. Iye anamva Yesu akulira mofuula kwa Atate wake. Anamvanso mawu omaliza omwe Yesu analankhula asanafe akuti, “ndakwaniritsa chifuniro chanu.” Mariya anakhumudwa kwambiri. Ngakhale zinali choncho, Yesu atafa, iye anakhalabe pomwepo. Ndipo kenako anakakhala pamanda atsopano omwe munthu wina wolemera wa ku Arimateya dzina lake Yosefe, anaikamo thupi la Yesu.—Yohane 19:30; Mateyu 27:45, 46, 57-61.

Zimene Mariya anachitazi zikutithandiza kudziwa zoyenera kuchita ngati Mkhristu mnzathu wakumana ndi mavuto. N’zoona kuti sitingathe kuchititsa kuti asakumane ndi mavuto kapena kumuchotsera mavutowo, koma tikhoza kumusonyeza chifundo komanso kumulimbikitsa. Komanso mnzathuyo angasangalale kwambiri kutiona kuti tilipo kuti timuthandize. Kukhala wokhulupirika pothandiza mnzathu amene ali m’mavuto kumasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro komanso kumalimbikitsa kwambiri mnzathuyo.—Miyambo 17:17.

Mayi ake a Yesu ayenera kuti anatonthozedwa kwambiri ataona kuti Mariya Mmagadala ali nawo limodzi

“Ine Ndikamutenga”

Thupi la Yesu litaikidwa m’manda, azimayi ena anakonza zoti akalipake zonunkhiritsa ndipo Mariya anali m’gulu limenelo. (Maliko 16:1, 2; Luka 23:54-56) Ndiye Sabata litatha, iye anadzuka m’mawa kwambiri. Tayerekezani kuti mukumuona ali ndi azimayi ena aja, akuyenda kunja kuli ka mdima kupita kumanda a Yesu. Ndiye azimayiwo akudzifunsa kuti akagubuduza bwanji chimwala chimene anatsekera khomo la mandawo. (Mateyu 28:1; Maliko 16:1-3) Komabe sanabwerere m’mbuyo. Chikhulupiriro chawo chinawachititsa kuchita zonse zimene akanatha n’kusiya zinazo m’manja mwa Yehova.

N’kutheka kuti Mariya anali patsogolo pa onse amene anakafika kumandawo. Koma kenako anangoima chilili ali odabwa. Mwala otsekera khomo la manda uja unali utachotsedwapo ndipo m’mandamo munalibe aliyense. Mariya sankazengereza pochita zinthu ndipo nthawi yomweyo akubwereranso akuthamanga kupita kwa Petulo ndi Yohane kukawauza zomwe anaonazo. Tayerekezani kuti mukumuona akufuulira atumwiwo mwaphuma kuti: “Ambuye awachotsa m’manda achikumbutso aja, ndipo sitikudziwa kumene awaika.” Nayenso Petulo ndi Yohane anathamangira kumandako ndipo anakatsimikiziradi kuti munalibe aliyense, kenako anabwerera kunyumba zawo. *Yohane 20:1-10.

Mariya atabwerera kumanda kuja, anakhalako yekhayekha. Unali m’mawa kwambiri ndipo kumandako kunali zii kopanda aliyense, moti Mariya ankangolira. Iye atasuzumira m’mandamo n’kuona kuti Ambuye mulibemo, sanamvetsebe ndipo anachita mantha. Kenako anaonamo angelo awiri ovala zoyera atakhala pansi. Iwo anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukulira?” Mariya anali atasokonezeka moti anabwereza mawu omwe anauza atumwi aja kuti: “Atenga Ambuye wanga, ndipo sindikudziwa kumene awaika.”—Yohane 20:11-13.

Atatembenuka anaona bambo wina ataima pafupi naye. Sanazindikire kuti anali ndani, ankangoganiza ngati anali munthu wosamalira mundawo. Bamboyo anamufunsa mwachifundo kuti: “Mayi iwe, n’chifukwa chiyani ukulira? Kodi Ukufuna ndani?” Iye anayankha kuti: “Bambo, ngati mwamuchotsa ndinu, ndiuzeni chonde kumene mwamuika, ndipo ine ndikamutenga.” (Yohane 20:14, 15) Taganizirani zimene anayankhazi. Kodi Mariya akanathadi kunyamula yekha thupi la Yesu Khristu, amene anali mwamuna wamphamvu komanso wathanzi? Mariya sanayambe waganizapo kaye zimenezi koma ankangoona kuti akufunika kuchita zomwe angathe.

“Ine ndikamutenga”

Kodi tingatsanzire bwanji Mariya Mmagadala pamene tili ndi chisoni kapena pamene takumana ndi mavuto enaake amene tikuona kuti sitingawapirire? Tikamangoganizira za zofooka zathu kapena zimene sitingakwanitse kuchita, tikhoza kukhala ndi mantha kwambiri moti tikhoza kulephera kuchitapo kanthu. Koma tikamayesetsa kuchita zonse zimene tingathe komanso kudalira Mulungu kuti atithandiza, tikhoza kukwanitsa kuchita zinthu zomwe sitinaziganizirepo n’komwe. (2 Akorinto 12:10; Afilipi 4:13) Ndipo koposa zonse, tidzasangalatsa Yehova. Zimenezi n’zomwe Mariya anachita ndipo Yehova anamudalitsa m’njira yapadera kwambiri.

“Ambuye Ndawaona Ine”

Bambo amene anaima pafupi ndi Mariya uja sanali wosamalira mundawo. Poyamba anali kalipentala, kenako mphunzitsi ndipo kenako anakhala Ambuye wokondedwa a Mariya. Komabe Mariya sanamuzindikire ndipo anayamba kubwerera. Iye sankakhulupirira zimene anauzidwa zoti Yesu waukitsidwa ndi thupi lauzimu. Koma Yesu anaonekera kwa Mariya ali ndi thupi la umunthu, osati limene anali nalo poyamba asanaphedwe. Inali nkhani yosangalatsa kwambiri Yesu ataukitsidwa. Komabe akaonekera kwa anthu, ngakhale amene ankamudziwa bwino poyamba, sankatha kumuzindikira.—Luka 24:13-16; Yohane 21:4.

Koma kodi Yesu anathandiza bwanji Mariya kuti amuzindikire? Iye anangomutchula dzina kuti: “Mariya!” Atamva zimenezi, iye anatembenuka ndi kuyankha m’Chiheberi mawu amene n’zosakayikitsa kuti ankakonda kuwagwiritsa ntchito polankhula ndi Yesu akuti “Rabboni!” Iye anazindikira kuti anali Mphunzitsi wake amene ankamukonda kwambiri. Mariya anasangalala kwambiri moti anamukangamira Yesu ndipo sanafune kumusiya.—Yohane 20:16.

Yesu anadziwa zolinga zake. Anamuuza kuti: “Usandikangamire.” Tikhoza kuona m’maganizo mwathu Yesu akuyankhula mawu amenewa mokoma mtima, mwinanso akumwetulira, uku akuchotsa manja a Mariya pang’onopang’ono n’kumuuza kuti: “Sindinakwerebe kwa Atate.” Nthawi yoti akwere kumwamba inali isanakwane. Anali adakali ndi ntchito yambiri padzikoli yoti achite ndipo ankafuna kuti Mariya azimuthandiza. Mariya anamvetsera chilichonse chimene Yesu ananena. Anamuuza kuti: “Pita kwa abale anga ukawauze kuti, ‘Ine ndikukwera kwa Atate wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.’”—Yohane 20:17.

Apatu Mariya analandira utumiki wapadera. Mariya anali ophunzira woyamba kumuona Yesu ataukitsidwa, ndipo apa tsopano Yesu akumupatsa mwayi wogwira ntchito youza ena uthenga wabwino. Mariya anasangalala kwambiri ndipo ankafunitsitsa kuuza ophunzira ena za uthenga umenewu. Mukhoza kumuona m’maganizo mwanu akupita kwa ophunzirawo mosangalala n’kuwauza kuti: “Ambuye ndawaona ine.” Iye anawafotokozera zonse zimene Yesu anamuuza ndipo ankalankhula mothamanga chifukwa cha chisangalalo. (Yohane 20:18) Zimene Mariya anafotokoza zinawonjezera pa zimene ophunzirawo anali atamva kale, kuchokera kwa azimayi ena amene anapita kukaona manda a Yesu aja.—Luka 24:1-3, 10.

“Ambuye ndawaona ine”

“Sanawakhulupirire Amayiwo”

Kodi atumwiwo anatani? Poyamba sanazikhulupirire. Baibulo limanena kuti: “Zimene anali kuwauzazo zinali zopanda pake ndipo sanawakhulupirire amayiwo.” (Luka 24:11) Amunawa anakulira m’dera limene anthu ake sankakhulupirira azimayi. Pa nthawi imeneyo, malamulo Achiyuda sankalola kuti azimayi azipereka umboni m’khoti. N’kutheka kuti atumwiwo anazindikira mochedwa kuti anatengera chikhalidwe chimenechi. Koma Yesu ndi Atate wake sachita zinthu mokondera. Ndipo umboni wake ndi zimene anachita popereka utumiki kwa mayi wokhulupirikayu.

Mariya sanakhumudwe ndi zimene amunawa anayankha. Iye ankadziwa kuti Ambuye wake amamudalira ndipo zinkamuchititsa kukhala wosangalala. Anthu onse amene amatsatira Yesu, anapatsidwa uthenga woti alengeze. Baibulo limanena kuti umenewu ndi “uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:1) Koma Yesu sanalonjeze otsatira akewo kuti anthu onse adzamvetsera kapena kukhulupirira uthengawo. M’malomwake anawauza zosiyana ndi zimenezi. (Yohane 15:20, 21) Choncho Akhristu onse akuyenera kumakumbukira chitsanzo cha Mariya Mmagadala. Ngakhale kuti ophunzira anzake sanakhulupirire uthenga wabwino umene anawauza, sizinamufooketse kapena kumulepheretsa kulengezabe za kuuka kwa Yesu.

Yesu anaonekera kwa atumwi ake ndipo kenako anaonekeranso kwa otsatira ake ena ambiri. Ulendo wina, anaonekera kwa anthu oposa 500 pa nthawi imodzi. (1 Akorinto 15:3-8) Chikhulupiriro cha Mariya chiyenera kuti chinkalimba kwambiri nthawi iliyonse imene Yesu waonekera kwa anthu, kaya iyeyo anali pompo kapena wangomva kwa anthu ena. N’kuthekanso kuti Mariya anali mmodzi mwa azimayi ena amene amatchulidwa kuti analipo pamsonkhano umene unachitika ku Yerusalemu, pa tsiku la Pentekosite pamene mzimu woyera unafikira otsatira a Yesu.—Machitidwe 1:14, 15; 2:1-4.

Sitikukayikira kuti Mariya Mmagadala anakhalabe wokhulupirika mpaka pamene anamwalira. Choncho tiyeni nafenso tiziyesetsa kutsanzira chikhulupiriro cha Mariya. Tizisonyeza kuyamikira zimene Yesu anatichitira, tiziyesetsa kugwira ntchito zooneka ngati zonyozeka potumikira ena komanso tizikhulupirira kuti Mulungu atithandiza.

^ ndime 17 Pa nthawi imene azimayi ena aja anakumana ndi mngelo amene anawauza kuti Yesu wauka kwa akufa, Mariya panalibepo. Akanakhala kuti analipo ndiye kuti akanauza Petulo ndi Yohane kuti mngelo wawafotokozera chifukwa chake thupi la Yesu lasowa.—Mateyu 28:2-4; Maliko 16:1-8.