Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Nkhawa?

Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Nkhawa?

Yankho la m’Baibulo

 Inde. Tikutero chifukwa chakuti Mulungu ndi amene angatithandize kwambiri. Pajatu Baibulo limati: “Mulungu, amene amatonthoza mtima wopsinjika, anatitonthoza ife mtima.”—2 Akorinto 7:6, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

Zimene Mulungu amapereka kuti atithandize

  •   Mphamvu. Mulungu ‘amatitonthoza’ poyankha mapemphero athu opempha mphamvu kuti tipirire osati pongochotsa mavutowo. (Afilipi 4:13) Musakayikire kuti Mulungu ndi wokonzeka kumvetsera mapemphero anu. Baibulo limati: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.” (Salimo 34:18) Mulungu amamvetsa zimene mukufuna kunena ngakhale pamene mukusowa mawu oti mufotokozere mmene mukumvera mumtima.—Aroma 8:26, 27.

  •   Zitsanzo za m’Baibulo. Munthu wina amene analemba nawo Baibulo anapemphera kuti: “Pa nthawi imene zinthu zinandivuta kwambiri ndinaitana pa inu.” Iye analimbikitsidwa atakumbukira kuti Mulungu amafunitsitsa kutikhululukira. Ananena kwa Mulungu kuti: “Mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova? Inu mumakhululukiradi, kuti anthu akuopeni.”—Salimo 130:1, 3, 4.

  •   Chiyembekezo. Masiku ano, Mulungu amatitonthoza komanso walonjeza kuti adzachotsa mavuto onse amene amatidetsa nkhawa. Zimenezi zikadzachitika, “zinthu zakale [monga nkhawa] sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.”—Yesaya 65:17.

 Dziwani izi: A Mboni za Yehova amadziwa kuti Mulungu amathandiza anthu amene ali ndi nkhawa koma nawonso amapita kuchipatala ngati akudwala matenda a maganizo. (Maliko 2:17) Sitilimbikitsa anthu kulandira chithandizo chinachake kuchipatala chifukwa munthu aliyense ayenera kusankha yekha pa nkhani ngati zimenezi.