Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Salimo 23:4​—“Ndingakhale Ndiyenda M’chigwa cha Mthunzi wa Imfa”

Salimo 23:4​—“Ndingakhale Ndiyenda M’chigwa cha Mthunzi wa Imfa”

 “Ngakhale ndikuyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani, sindikuopa kanthu, pakuti inu muli ndi ine. Chibonga chanu ndi ndodo yanu ndi zimene zimandilimbikitsa.”​—Salimo 23:4, Baibulo la Dziko Latsopano.

“Inde, ndingakhale ndiyenda m’chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine: Chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.​—Salimo 23:4, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Salimo 23:4 a

 Mulungu amasamalira komanso kuteteza anthu amene amamulambira, ngakhale pamene akumana ndi mavuto aakulu. Vesili limayerekezera mmene Mulungu amasamalirira anthu ake ndi mmene m’busa amasamalirira nkhosa zake. b Anthu ake samaona kuti ali okha akakumana ndi mavuto, omwe pavesili ayerekezeredwa ndi mdima wandiweyani kapena nthawi imene moyo uli pa ngozi. Iwo amaona kuti ndi otetezeka ngati kuti Mulungu ali nawo pafupi.

 Kale, m’busa ankagwiritsa ntchito ndodo kapena chibonga kuti aziteteza nkhosa ku zinyama zolusa. Iye ankagwiritsanso ntchito ndodo yake, yomwe inali yokhota kumapeto, kuti azikusira nkhosa kapena kuwakoka kuti achoka pazinthu zoopsa. Mofananamo, Yehova Mulungu ali ngati m’busa wachikondi amene amateteza komanso kutsogolera anthu amene amamulambira. Ngakhale pa nthawi yovuta kwambiri, Yehova amawasamalira m’njira zosiyanasiyana.

  •   Iye amawalangiza komanso kuwalimbikitsa pogwiritsa ntchito Mawu ake, Baibulo.​—Aroma 15:4.

  •   Amamvetsera mapemphero awo ndipo amawathandiza kuti maganizo awo akhale pansi n’kuwapatsa mtendere wamumtima.​—Afilipi 4:6, 7.

  •   Amagwiritsanso ntchito Akhristu anzawo kuti aziwalimbikitsa anthu ake.​—Aheberi 10:24, 25.

  •   Amalonjeza kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo ndipo iye adzachotsa mavuto awo onse.​—Salimo 37:29; Chivumbulutso 21:3-5.

Nkhani yonse ya Salimo 23:4

 Salimo 23 linalembedwa ndi Davide, yemwe ali wamng’ono anali m’busa ndipo anadzakhala mfumu ya Isiraeli. (1 Samueli 17:34, 35; 2 Samueli 7:8) Salimoli limayamba ndi mawu ofotokoza Yehova ngati M’busa yemwe amatsogolera, kudyetsa komanso kutsitsimutsa anthu ake ngati mmene m’busa weniweni amachitira ndi nkhosa zake.​—Salimo 23:1-3.

 Pa Salimo 23:4, pamene Davide ankafotokoza za mmene Mulungu amatitetezera, anasiya kufotokoza Mulungu pogwiritsa ntchito mawu oti “iye” n’kuyamba kugwiritsa ntchito mawu oti “inu.” Kusinthaku kumasonyeza kuti Davide anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Davide ankadziwa kuti Mulungu ankamuganizira komanso kudziwa bwino mavuto ake. Choncho Davide sankaopa chilichonse.

 Mavesi otsatira mu Salimo 23, omwe ndi vesi 5 ndi 6, sanena za m’busa ndi nkhosa zake koma za munthu ndi mlendo wake. Mofanana ndi munthu wochereza alendo, Yehova amachita zinthu ndi Davide ngati kuti ndi mlendo wolemekezeka. Ngakhale adani a Davide sankatha kulepheretsa kuti Mulungu azimusamalira Davideyo. Pavesi lomaliza la Salimoli, Davide anasonyeza kuti sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Mulungu adzamuchitira zabwino komanso kumusonyeza chikondi mpaka moyo wake wonse.

 Mawu ophiphiritsa a mu Salimo 23 amasonyeza kuti nthawi zonse Mulungu amasamalira anthu ake mwachikondi.​—1 Petulo 2:25.

a M’Mabaibulo ena Salimoli ndi Salimo 22. Pali masalimo 150 ndipo Mabaibulo ena amawawerengera mogwirizana ndi Malemba a Chiheberi omwe Amasorete anakopera. Koma Mabaibulo ena amawawerengera mogwirizana ndi Baibulo la Septuagint, limene ndi Malemba a Chiheberi omasuliridwa m’Chigiriki lomwe linamalizidwa kulembedwa m’zaka za m’ma 100 B.C.E.

b Mulungu, yemwe dzina lake ndi Yehova, nthawi zambiri amayerekezeredwa ndi M’busa wachikondi m’Baibulo. Anthu ake, omwe amayerekezeredwa ndi nkhosa, amamudalira kuti aziwateteza komanso kuwasamalira.​—Salimo 100:3; Yesaya 40:10, 11; Yeremiya 31:10; Ezekieli 34:11-16.