Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Zolaula? Kodi N’kulakwa Kulankhulana Zokhudza Kugonana pa Intaneti?

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Zolaula? Kodi N’kulakwa Kulankhulana Zokhudza Kugonana pa Intaneti?

Yankho la m’Baibulo

 M’Baibulo mulibe mawu akuti zolaula kapena kutumizirana mauthenga okhudza kugonana. Komabe Baibulo limanena momveka bwino mmene Mulungu amaonera chilichonse chimene chimalimbikitsa zoti anthu azigonana ndi munthu yemwe sanakwatirane naye kapenanso chinthu chilichonse chimene chimalimbikitsa maganizo olakwika pa nkhani yogonana. Taonani mavesi a m’Baibulo otsatirawa:

  •   “Chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana.” (Akolose 3:5) M’malo mochititsa kuti chilakolako chogonana chikhale chakufa, kuonerera zolaula kumaonjezera chilakolako chimenechi. Kuonerera zolaula kumachititsa munthu kuti akhale wodetsedwa m’maso mwa Mulungu.

  •   “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28) Zithunzi zolaula zimachititsa munthu kuti akhale ndi maganizo olakwika omwe angachititse munthuyo kuchita zinthu zoipa.

  •   “Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu.” (Aefeso 5:3) Ngati sitikuyenera n’komwe kutchula zinthu zokhudza kugonana pofuna kungosangalala, n’zachidziwikire kuti sitikuyeneranso kuwonerera zolaula.

  •   “Ntchito za thupi zimaonekera. Ntchitozi ndizo dama, zinthu zodetsa, . . . ndi zina zotero. Ponena za zinthu zimenezi, ndikukuchenjezeranitu, ngati mmene ndinachitira poyamba paja, kuti anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (Agalatiya 5:​19-21) Mulungu amaona kuti anthu onse amene amaonerera zolaula kapena amene amatumizirana mauthenga okhudza zogonana, ndi odetsedwa. Ngati timakonda kuonerera zolaula kapenanso kutumizirana mauthenga okhudza zogonana, Mulungu angasiyiretu kutikonda.