Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani pa Nkhani Yotumizirana Mameseji ndi Zinthu Zina Zolaula?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani pa Nkhani Yotumizirana Mameseji ndi Zinthu Zina Zolaula?

 N’chifukwa chiyani anthu ena amatumizirana zolaula?

 Anthu amatumizirana mameseji okhudza kugonana, zithunzi kapena mavidiyo olaula pogwiritsira ntchito foni ya m’manja. Munthu wina ananena kuti: “Masiku ano anthu ambiri akuona kuti imeneyi ndi njira yochezera basi. Zimayamba ndi kutumizirana mameseji kenako mumayamba kutumizirana zithunzi zolaula.”

 Koma n’chifukwa chiyani anthu amatumizirana zolaula? Achinyamata ena amaona kuti “kukhala ndi chithunzi cha maliseche cha munthu amene uli naye pachibwenzi zimasonyeza kuti ndiwe mkazi kapena mwamuna weniweni.” Anatero loya wa boma m’nyuzipepala yotchedwa The New York Times. Wachinyamata wina anafika ponena kuti kutumizirana zolaula ndi “njira yabwino yogonanira chifukwa sungatenge mimba kapena matenda opatsirana pogonana.”

 Taonani zifukwa zinanso zimene achinyamata amatumizirana zolaula:

  •   Kuti akope munthu amene amafuna atakhala naye pachibwenzi.

  •   Munthu wina amakhala kuti wawatumizira chithunzi cholaula, ndiye nawonso amafuna kuti atumize chawo posonyeza kuyamikira.

 Kodi ndi mavuto ati amene amakhalapo chifukwa chotumizirana zolaula?

 Mukatumiza chithunzi pa foni ya m’manja, chimakhala kuti chapita basi ndipo simungadziwe kuti amene wachilandirayo achita nacho zotani. Simudziwanso kuti zikhudza bwanji mbiri yanu. Katswiri wina dzina lake Amanda Lenhart, yemwe anachita kafukufuku pa nkhaniyi mogwirizana ndi bungwe la Pew Research Center, analemba mulipoti lake kuti: “Zimakhala zosavuta kugwiritsa ntchito mameseji olaula ngati umboni woti munthu anachita khalidwe loipa. Izi zili choncho chifukwa mameseji amatha kusungidwa komanso kutumizidwa kwa anthu ena mosavuta.”

 Nthawi zina

  •    Munthu amene walandira zithunzi za maliseche amatha kutumizanso zithunzizo kwa anzake pofuna kuwasangalatsa.

  •    Mtsikana akathetsa chibwenzi, mnyamata yemwe anali naye pa chibwenziyo amabwezera chipongwe potumizira anthu ena zithunzi zamaliseche za mtsikanayo.

 KODI MUKUDZIWA? Nthawi zambiri, anthu omwe amatumizirana zithunzi zamaliseche amaonedwa kuti apalamula mlandu wofanana ndi kugwiririra ana kapena kuwachitira nkhanza m’njira zina. Anthu otero angaonedwenso kuti akupalamula mlandu wofanana ndi kutumiza zithunzi za ana zamaliseche. Ndipotu ana ena amene ankatumizirana zolaula anaimbidwa milandu yofanana ndi kugwiririra.

 Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?

 Baibulo limasonyeza kuti anthu okwatirana okha ndi amene ayenera kugonana. (Miyambo 5:18) Koma limanena mosapita m’mbali kuti anthu omwe sanakwatirane sakuyenera kumagonana. Taonani mavesi a m’Baibulo otsatirawa:

  •  “Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu, . . . musatchule ngakhale za khalidwe lochititsa manyazi, nkhani zopusa kapena nthabwala zotukwana.”—Aefeso 5:3, 4.

  •  “Chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje.”—Akolose 3:5.

 Mavesiwa sikuti akungoletsa “dama” (kugonana kwa anthu amene sanakwatirane) koma akuletsanso zinthu zina. Mwachitsanzo, akuletsa “zinthu zodetsa” (zomwe ndi khalidwe lililonse loipa komanso lodetsa) ndi “chilakolako cha kugonana” (osati chikondi chimene anthu okwatirana amasonyezana m’banja koma chilakolako choipa chimene chingapangitse munthu kuchita khalidwe loipa).

 Dzifunseni kuti:

  •   N’chifukwa chiyani kutumizirana zithunzi za maliseche kuli m’gulu la “zinthu zodetsa”?

  •   Kodi zimalimbikitsa bwanji ‘chilakolako choipa cha kugonana’?

  •   N’chifukwa chiyani mtima wofuna kuona kapena kutumiza zithunzi za maliseche ndi ‘woipa’ kwambiri?

 Mavesi a m’Baibulo otsatirawa akupereka zifukwa zinanso zimene zikutilimbikitsa kupewa kutumizirana zolaula.

  •   “Chita chilichonse chotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomerezeka pamaso pa Mulungu, wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi.”—2 Timoteyo 2:15.

  •    “Ganizirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu.”—2 Petulo 3:11.

 Mavesiwa akufotokoza ubwino wokhala ndi khalidwe loyera. Mukakhala ndi khalidwe labwino, simukhala ndi nkhawa yakuti zochita zanu tsiku lina zidzakutsatani.​—Agalatiya 6:7.

 Dzifunseni kuti:

  •    Kodi ndine munthu wotani?

  •    Kodi ndimapewa kuipitsa mbiri ya anthu ena?

  •    Kodi ndimafuna kusangalala ndi zinthu zimene zingakhumudwitse ena?

  •    Kodi kutumizirana zolaula kungawononge bwanji mbiri yanga?

  •    Kodi kutumizirana zolaula kungapangitse bwanji kuti makolo anga asiye kundikhulupirira?

 NKHANI IMENE INACHITIKADI “Ndili ndi mnzanga amene anali pachibwenzi cha mseri ndi mnyamata winawake. Iye anatumiza chithunzi chake chamaliseche kwa mnyamatayo, ndipo naye mnyamatayo anatumizanso chake. Koma pasanathe n’komwe masiku awiri, bambo a mtsikanayo anaganiza zoona foni yake. Iwo sanakhulupirire ataona mameseji amene anali mufoniyo. Anamufunsa za mamesejiwo ndipo mtsikanayo sanakane chilichonse. Ndikudziwa kuti anavomereza kuti walakwadi, koma makolo ake anakhumudwa kwambiri chifukwa sankayembekezera kuti iye angamatumizirane zithunzi zamaliseche ndi mnyamata. Mpaka pano makolo ake amamukayikirabe.”

 Mfundo yoona: Kutumizirana zolaula kumakhudza wotumizayo komanso wolandira. Mnyamata wina anakakamiza mtsikana amene anali naye pachibwenzi kuti azitumizirana zithunzi zolaula. Mtsikanayo ananena kuti: “Kutumizirana zolaula kumandichititsa kuti ndizidziona ngati ndikuyenda mbulanda komanso ngati ndine wopanda ntchito.”

 Popeza kutumizirana zolaula kungabweretse mavuto kwa inuyo, anthu ena, komanso mwina mungaimbidwe mlandu ndi boma, ndi bwino kuti muzitsatira malangizo a m’Baibulo awa:

 Inuyo mungachite chiyani?

 Onani mmene mungagwiritsire ntchito malangizo a m’Baibulo pa zochitika zenizeni pa moyo. Werengani zimene Janet ananena kenako sankhani zimene mukuona kuti ndi njira yabwino kwambiri kutsatira.

 “Nthawi ina ndinakumana ndi mnyamata ndipo tinapatsana manambala a foni. Mlungu umodzi usanathe, anayamba kundiuza kuti ndimutumizire chithunzi changa nditavala zamkati zokha.”​—Janet.

 Kodi mukuganiza kuti Janet anayenera kuchita chiyani? Nanga inuyo mukanatani?

  •  A: Mukanaganiza kuti, ‘Palibe vuto lililonse kumutumizira. Ndipo tikadzapita kunyanja adzandionabe nditavala zovala zamkati zokha.’

  •  B: Mukanaganiza kuti, ‘Sindikudziwa kuti cholinga chake n’chiyani. Ndingotumiza chithunzi chosonyeza ineyo nditavala bwino ndithu kuti ndione zimene angachite.’

  •  C: Mukanaganiza kuti, ‘Mnyamatayu akungofuna kugonana basi. Ndikufufuta meseji yakeyi.’

 Yankho la C likuoneka kuti ndi lolondola eti? Ndipotu Baibulo limanena kuti: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.”—Miyambo 22:3.

 Zimene zinachitikira Janet zikutithandiza kuona zimene nthawi zambiri zimayambitsa khalidwe lotumizirana zolaula komanso makhalidwe ena oipa. Nkhani yagona pa anthu ocheza nawo. Kodi inuyo mumasankha mwanzeru anthu ocheza nawo? (Miyambo 13:20) Mtsikana wina dzina lake Sarah anati: “Muzicheza ndi anthu amene mukudziwa kuti sangasekerere khalidwe loipa.” Mtsikana winanso dzina lake Delia ananena kuti: “Anthu ena amene timawaona kuti ndi anzathu amatilimbikitsa kuti tikhale ndi makhalidwe oipa m’malo motithandiza kuti tikhale ndi makhalidwe abwino. Ngati amachita zinthu zosiyana ndi zimene Mulungu amafuna, ndiye kuti akukulimbikitsa kuti uzichita zinthu zimene ukudziwa kuti ndi zoipa. Anthu otere si abwino kucheza nawo.”