Miyambo 5:1-23

  • Chenjezo lokhudza akazi amakhalidwe oipa (1-14)

  • Sangalala ndi mkazi wako (15-23)

5  Mwana wanga, tchera makutu ako ku mawu anga anzeru. Mvetsera mosamala zimene ndikukuphunzitsa zokhudza kukhala wozindikira,+   Kuti uteteze luso lako loganiza bwino,Ndiponso kuti milomo yako iteteze kudziwa zinthu.+   Chifukwa milomo ya mkazi wamakhalidwe oipa* imakha uchi ngati chisa cha njuchi,+Ndipo mʼkamwa mwake ndi mosalala kuposa mafuta.+   Koma pamapeto pake amawawa kwambiri ngati chitsamba chowawa.+Ndipo amakhala wakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.+   Mapazi ake amatsikira ku imfa. Miyendo yake imalowera ku Manda.*   Iye saganizira zimene zingamuthandize kukapeza moyo. Amangoyendayenda, osadziwa kumene akulowera.   Tsopano mwana wanga,* ndimvere,Ndipo usapatuke pa zimene ndikukuuza.   Ukhale kutali kwambiri ndi iye.Usayandikire pakhomo la nyumba yake,+   Kuti usapereke ulemu wako kwa anthu ena+Komanso kuti usakumane ndi mavuto mʼzaka zotsala za moyo wako.*+ 10  Ndiponso kuti alendo asakuwonongere zinthu zako,*+Komanso kuti zinthu zimene unazipeza movutikira zisapite kunyumba ya mlendo. 11  Ukapanda kumvera, udzabuula kumapeto kwa moyo wako,Mphamvu zako zikadzatha komanso ukadzawonda kwambiri.+ 12  Ndipo udzanena kuti: “Ndinkadana ndi malangizo* ine! Ndipo mtima wanga sunkamvera, ena akandidzudzula. 13  Sindinamvere mawu a alangizi anga,Kapena kutchera khutu kwa aphunzitsi anga. 14  Ndangotsala pangʼono kutheratuPakati pa mpingo wonse.”*+ 15  Imwa madzi ochokera mʼchitsime chako,Komanso madzi oyenderera kuchokera pakasupe wako.+ 16  Kodi akasupe ako amwazike panja?Ndipo kodi mitsinje yako ya madzi imwazike mʼmabwalo amumzinda?+ 17  Zimenezi zikhale zako zokhaosati uzigawana ndi anthu achilendo.+ 18  Kasupe wako akhale wodalitsidwa,*Ndipo uzisangalala ndi mkazi amene unamukwatira udakali wachinyamata.+ 19  Iye akhale ngati mbawala yaikazi yachikondi komanso ngati kamwana ka mbuzi zamʼmapiri kokongola.+ Mabere ake azikukhutiritsa* nthawi zonse. Chikondi chake chizikusangalatsa kwambiri nthawi zonse.+ 20  Ndiye mwana wanga, kodi pali chifukwa chilichonse choti uzisangalalira ndi mkazi wamakhalidwe oipa,*Kapena choti uzikumbatirira chifuwa cha mkazi wachiwerewere?*+ 21  Chifukwa maso a Yehova amaona chilichonse chimene munthu akuchita,Ndipo iye amafufuza njira zake zonse.+ 22  Woipa amakodwa ndi zolakwa zake zomwe,Ndipo adzamangidwa ndi zingwe za tchimo lake lomwe.+ 23  Iye adzafa chifukwa chosamvera malangizo,Ndipo adzasochera chifukwa cha kuchuluka kwa uchitsiru wake.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana anga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti usapereke zaka zako ku zinthu zankhanza.”
Kapena kuti, “mphamvu zako.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Pakati pa msonkhano komanso mpingo.”
Kapena kuti, “Pamene umatunga madzi ako pakhale podalitsidwa.”
Kapena kuti, “azikusangalatsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”