Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Yohane 16:33​—“Ndaligonjetsa Dziko”

Yohane 16:33​—“Ndaligonjetsa Dziko”

 “Ndanena zimenezi kwa inu kuti mukhale mu mtendere chifukwa cha ine. M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.”​—Yohane 16:33, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M’dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndaligonjetsa dziko lapansi Ine.​—Yohane 16:33, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Zimene lemba la Yohane 16:33 limatanthauza

 Yesu ananena mawuwa potsimikizira otsatira ake kuti nawonso angakwanitse kusangalatsa Mulungu ngakhale atakumana ndi mayesero kapena kutsutsidwa.

 “Ndanena zimenezi kwa inu kuti mukhale mu mtendere chifukwa cha ine.” a Mawu ena a muvesili akusonyeza kuti kukhala mu mtenderewu sikutanthauza kusakumana ndi mavuto. Koma akutanthauza kukhala ndi mtendere wamumtima. Munthu angakhale ndi mtendere wa mumtimawu “chifukwa cha” Yesu, yemwe analonjeza kuti adzatumiza mzimu woyera. Mzimuwo womwe ndi “Mthandizi” wamphamvu, umathandiza ophunzira a Yesu kuti zinthu ziwayendere bwino ngakhale atakumana ndi mavuto.​—Yohane 14:16, 26, 27.

 “M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima.” Yesu ananena mosapita m’mbali kuti ophunzira ake adzakumana ndi mayesero, monga kuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo komanso kuzunzidwa. (Mateyu 24:9; 2 Timoteyo 3:12) Ngakhale zinali choncho, ophunzirawo anali ndi chifukwa chomveka chokhalira ‘olimba mtima.’​—1 Yohane 2:15-17.

 “Ine ndaligonjetsa dziko.” Palembali, mawu oti “dziko” akunena za anthu oipa omwe sasangalatsa Mulungu. b Lemba la 1 Yohane 5:19 limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo,” kapena kuti Satana. N’chifukwa chake anthu am’dzikoli amachita zinthu zosemphana ndi zimene Mulungu amafuna.​—1 Yohane 2:15-17.

 Satana ndi dziko lake ankayesetsa kulepheretsa Yesu kuchita zimene Mulungu ankafuna, zomwe zinkaphatikizapo kuphunzitsa ena zokhudza Mulungu komanso kupereka moyo wake wangwiro monga nsembe. (Mateyu 20:28; Luka 4:13; Yohane 18:37) Koma Yesu sanalole kuti maganizo a m’dzikoli amulepheretse kuchita zimene Mulungu ankafuna. Iye anakhalabe wokhulupirika mpaka imfa. Choncho ndi pomveka kuti iye ananena kuti analigonjetsa dziko komanso kuti Satana, amene ndi “wolamulira wa dziko,” analibe ‘mphamvu pa iye.’​—Yohane 14:30.

 Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo chake posonyeza otsatira ake kuti nawonso akhoza kukhala okhulupirika kwa Mulungu ngakhale atakumana ndi mayesero. Zinali ngati kuti Yesu akunena kuti: “Ngati ndingagonjetse dziko, inunso mukhoza kuligonjetsa.”

Zomwe zinachititsa Yesu kunena mawu a pa Yohane 16:33

 Yesu ananena mawuwa usiku woti aphedwa mawa lake. Podziwa kuti watsala pang’ono kuphedwa, anagwiritsa ntchito mpatawu kuti apereke malangizo omaliza kwa atumwi ake okhulupirika. M’malangizowo, anawauza mfundo zimene atumwiwo ankafunika kuziganizira mozama. Anawauza kuti sadzawaonanso komanso kuti adzazunzidwa ngakhalenso kuphedwa kumene. (Yohane 15:20; 16:2, 10) Podziwa kuti mfundozi zikanachititsa mantha atumwiwo, Yesu anamaliza ndi mawu a pa Yohane 16:33 n’cholinga choti awalimbikitse.

 Mawu a Yesuwa komanso chitsanzo chake zingalimbikitsenso otsatira ake masiku ano. Akhristu onse angakhale okhulupirika kwa Mulungu ngakhale atakumana ndi mayesero.

a Mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti “chifukwa cha ine” angamasuliridwenso kuti “mogwirizana ndi ine.” Mawuwa amasonyeza kuti ophunzira a Yesu angakhale ndi mtendere akamachita zinthu mogwirizana ndi Yesuyo.

b Mawu oti “dziko,” amatchulidwanso pa Yohane 15:19 ndi pa 2 Petulo 2:5 ndipo tanthauzo lake ndi lofanana.