Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuphunzila kugwila nchito molimbika kuli monga kucita maseŵela olimbitsa thupi. Kungakupinduliseni lomba komanso m’tsogolo

KWA ACICEPELE

11: Kukhala Wolimbika

11: Kukhala Wolimbika

ZIMENE KUMATANTHAUZA

Anthu olimbika sapewa kugwila nchito. M’malo mwake, iwo amakondwela kugwila nchito mwamphamvu kuti apeze zofunikila mu umoyo wawo na kuthandizanso ena. Amacita izi olo kuti nchito imene amagwila siyokhumbilika.

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA

Tifune, tisafune, munthu aliyense wa moyo amafunika kugwila nchito. Kukhala wolimbikila nchito n’kopindulitsa m’njila zambili cifukwa cakuti anthu ambili m’dzikoli ni osalimbika pa nchito.—Mlaliki 3:13.

“Naphunzila kuti ngati ugwila nchito molimbika, umakhala wacimwemwe komanso wokhutila. Kudzimva wokhutila kwanithandiza kuti nizikonda nchito. Kugwila nchito molimbika kudzakuthandizaninso kukhala na mbili yabwino.”—Reyon.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Kugwila nchito iliyonse [mwakhama] kumapindulitsa.”—Miyambo 14:23.

ZIMENE MUNGACITE

Kuti muyambe kuona nchito moyenela, mungacite zotsatilazi:

Pezani cimwemwe mwa kuwonjezela luso pa nchito. Kaya mucita homuweki, mugwila nchito za pakhomo, kapena mugwila nchito ina iliyonse yakuthupi, muziicita ndi mtima wonse. Mukayamba kuigwila bwino nchito imene mwapatsidwa, muzionanso mbali zimene mungaongolele kuti ulendo wotsatila mukaicite bwino kwambili komanso mwamsanga. Pamene mukulitsa luso pa nchito yanu, m’pamenenso mudzakondwela nayo kwambili.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Kodi wamuona munthu waluso pa nchito yake? Iye adzaima pamaso pa mafumu. Sadzaima pamaso pa anthu wamba.”—Miyambo 22:29.

Ganizilani mmene nchito yanu imapindulitsila ena. Nthawi zambili, pamene mumagwila bwino nchito zimene mwapatsidwa, mumapindulitsanso ena. Mwacitsanzo, ngati mumalimbikila kugwila nchito za pakhomo, mumapeputsilako ena zocita m’banja lanu.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.”—Machitidwe 20:35.

Muzicita zoposa zimene mwauzidwa kucita. M’malo mocita cabe zimene mwapemphedwa, muziyesetsa kucita mopitililapo. Mwa njila imeneyi, ndiye kuti mudziphunzitsa kucita zinthu zoposa pa zimene muyembekezeleka kucita, osati kucita kukukakamizani koma mwa kufuna kwanu.—Mateyu 5:41.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Cabwino cimene ungacite cisakhale cokukakamiza, koma ucite mwa kufuna kwa mtima wako.”—Filimoni 14.

Muzigwila nchito mwa cikati-kati. Anthu olimbika amapewanso kugwila nchito mopitilila malile. Iwo amacita zinthu mwacikati-kati ndipo amapeza cimwemwe ponse paŵili, pogwila nchito komanso panthawi yopumula.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwila nchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”—Mlaliki 4:6.