Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kukhululukilana kungazimitse mikangano imene ili ngati moto

KWA OKWATILANA

4: Kukhululukilana

4: Kukhululukilana

ZIMENE KUMATANTHAUZA

Kukhululuka kumatanthauza kuiŵalako zimene wina watilakwila na kusasunga cakukhosi. Sikutanthauza kucepetsa colakwaco, kapena kuciona monga kuti sicinacitike.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake.”—Akolose 3:13.

“Ngati umakonda mnzako, suika kwambili maganizo ako pa zimene amalakwitsa, koma umaona zimene amacita poyesetsa kukhala munthu wabwino.”—Aaron.

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA

Ngati musunga cakukhosi, mungaononge thanzi lanu komanso cikwati canu.

“Tsiku lina mwamuna wanga anapepesa pa zimene anacita zonikhumudwitsa kwambili. Poyamba zinanivuta kuti nim’khululukile. N’zoona kuti pambuyo pake n’namukhululukila, koma nimadziimba mlandu kuti n’nacedwa kucita zimenezo. Cifukwa zinapangitsa kuti mgwilizano wathu usokonezeke kwa kanthawi pa zifukwa zosamveka.”—Julia.

ZIMENE MUNGACITE

DZIFUFUZENI

Nthawi ina ngati mnzanu wa m’cikwati wacitanso zinthu kapena wakamba mau amene akukhumudwitsani, mukadzifunse kuti:

  • ‘Kodi nimakalipa msanga?’

  • ‘Kodi wanilakwila kwambili cakuti afunika kunipepesa, kapena niiŵaleko cabe?’

KAMBILANANI NA MNZANU WA M’CIKWATI

  • Kodi zimatitengela nthawi yaitali bwanji kuti tikhululukilane?

  • Kodi tingacite ciani kuti tizikhululukilana msanga?

MUNGACITENSO IZI

  • Mnzanu wa m’cikwati akakulakwilani, pewani kukaikila zolinga zake.

  • Muzim’khululukila mnzanu wa m’cikwati, podziwa kuti “tonsefe timapunthwa nthawi zambili.”—Yakobo 3:2.

“Cimakhala copepuka kukhululukilana ngati nonse aŵili mwalakwitsa, koma cimakhala covuta ngati mmodzi ndiye walakwitsa. Kulandila cipepeso na kukhululuka kumafuna kudzicepetsa kwambili.”—Kimberly.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Thetsa nkhani mofulumila.”—Mateyu 5:25.

Ngati musunga cakukhosi, mungaononge thanzi lanu komanso cikwati canu