Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Zolinga zili monga pulani. Mukalimbikila, mungazikwanilitse

KWA ACICEPELE

12: Zolinga

12: Zolinga

TANTHAUZO LAKE

Zolinga sizili monga maloto cabe amene ungakonde kuti acitike. Koma zolinga zeni-zeni zimafuna kukonzekela, kukhala wokonzeka kusintha, komanso paja amati kanthu n’khama.

Zolinga zingakwanilitsidwe m’nthawi yocepa (zotenga masiku kapena ma wiki kuti zikwanilitsidwe), kapena m’nthawi yotalikilapo pang’ono (miyezi), komanso zotenga nthawi yaitali (caka kapena kupitililapo). Zolinga zikulu-zikulu zotenga nthawi yaitali zingakwanilitsidwe mwa kudziikila zolinga zina zing’ono-zing’ono na kuzikwanilitsa.

CIFUKWA CAKE N’ZOFUNIKA

Kukwanilitsa zolinga kungakuthandizeni kuti musamadzikayikile, mulimbitse maubwenzi anu, ndiponso muwonjezele cimwemwe canu.

Kusadzikayikila: Mukadziikila zolinga zing’ono-zing’ono na kuzikwanilitsa, mumalimba mtima kuti mungakwanilitsenso zolinga zikulu-zikulu. Mumakhalanso na mphamvu yolimbana ndi zopinga za tsiku na tsiku. Mwacitsanzo, mumatha kukana kutunthiwa na anzanu.

Mabwenzi: Anthu amakondwela kuceza komanso kugwila nchito ndi anthu amene ali na zolinga mu umoyo wawo, amenenso amayesetsa kuzikwanilitsa. Kuonjezela apo, imodzi mwa njila zimene mungalimbitsile ubwenzi na munthu ni mwa kucitila naye zinthu pamodzi kuti mukwanilitse colinga cina cake.

Cimwemwe: Mukadziikila zolinga na kuzikwanilitsa mumamvela bwino mu mtima podziŵa kuti mwacita zimene munali kufuna.

“Nimakonda kukhala na zolinga. Zimanipangitsa kukhala bize podziŵa kuti nifunika kukwanilitsa colinga cina cake. Ndipo ukacikwanilitsa, umamvela bwino na kudziuza kuti, ‘Yaa, nacita zimene n’nali kufuna! Nakwanilitsa colinga canga.’”—Christopher.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Woyang’ana mphepo sadzabzala mbewu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.”—Mlaliki 11:4.

ZIMENE MUNGACITE

Citani zotsatilazi kuti mudziikile zolinga na kuzikwanilitsa.

Sankhani zolinga zimene mungazikwanilitse. Lembani mndandanda wa zolinga zimene mungafune kuzikwanilitsa motsatila kufunika kwake. Zina mungaziike pa malo oyamba, aciŵili, acitatu mpaka conco.

Konzekelani. Pa colinga ciliconse cimene mwalemba, citani zotsatilazi:

  • Ikani deti yothela yocikwanilitsila.

  • Onani masitepu ofunikila kutenga.

  • Ganizilani zopinga zimene mungakumane nazo ndi mmene mungazigonjetsele.

Yambani kucitapo kanthu. Mukadziikila zolinga, yambani kuseŵenzelapo mwamsanga. Musayembekezele kuti zonse zikhale m’malo. Dzifunseni kuti, ‘Kodi cinthu coyamba cimene nifunika kucita kuti nikwanilitse colinga canga n’ciani?’ Mukacidziŵa, ciciteni. Pamene nthawi ikuyenda, muzipatula nthawi yoonanso zimene mwacitako pofuna kukwanilitsa colinga canu.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulila.”—Miyambo 21:5.