Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Sadzachedwa” (Nyimbo ya Msonkhano wa 2023)

“Sadzachedwa” (Nyimbo ya Msonkhano wa 2023)

(Habakuku 2:3)

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Dziko lopanda nkhawa zonsezi

    Ndi lomwe tonse tikulakalaka. 

    Padziko lonse zinthu zaipa 

    Tikudziwatu muthetsa zonsezi. 

    (KOLASI)

    Molezadi mtima tikudikirira

    Dzikotu latsopano. 

    Mapeto afika posachedwa pompa. 

    Mawu anu akuti, ‘sadzachedwadi.’ 

  2. 2. Mulungu wathu mudzaitana

    Omwe anafa, ndipo adzadzuka. 

    Zidzakhalatu zosangalatsa! 

    Tithandizeni kulezabe mtima. 

    (KOLASI)

    Molezadi mtima tikudikirira

    Dzikotu latsopano. 

    Mapeto afika posachedwa pompa. 

    Mawu anu akuti, ‘sadzachedwadi.’ 

  3. 3. Mumafufuza mitima yathu 

    N’kutitonthoza ndi chiyembekezo. 

    Tichite khama polalikira. 

    Tikhale maso nthawi yafupika. 

    (KOLASI)

    Molezadi mtima tikudikirira

    Dzikotu latsopano. 

    Mapeto afika posachedwa pompa. 

    Mawu anu akuti, ‘sadzachedwadi.’ 

    Tiyembekezerebe. 

(Onaninso Akol. 1:11.)