Ndife Banja Limodzi
Pangani Dawunilodi:
1. Tafika mu dziko lina
Tachokeratu kutali
Kuno sikwathu
Koma Yehova
Akutithandizadi.
Ntchitoyi ingativute ndithu,
Koma ndi ya Yehova.
Timakondanso abale ndi mtima wonse,
Tikunena kuti:
(KOLASI)
Tonse ndi a Yehova
Ndifedi banja limodzi
Kwanu kutalike bwanji,
Ndifedi
Banja limodzi.
2. Mwatichingamira ndithu,
Mwatilandilatu bwino.
Nyimbo zayamba pa msokhanowu,
Chikondi chikukula.
Tikudziwa ndi Yehova yekha
Angachititse izi.
Tim’tamande, timukonde mpaka kale
Ku madera onse.
(KOLASI)
Tonse ndi a Yehova
Ndifedi banja limodzi
Kwanu kutalike bwanji,
Ndifedi
Banja limodzi.
3. Mu ndege, tadutsa nyanja
Kuno tafika n’kutali.
Tilalikire, anthu abwino
Omwe tawapezawa.
Tikumva ngatitu tili kwathu
N’chikondi cha abale.
Timakonda ubale wa padziko lonse,
Kuli konseko.
(VESI LOKOMETSERA)
Tikudziwa
Timakapeza ’bale kulikonse,
Mali mpaka Mexico,
Japan mpaka Jamaica.
(KOLASI)
Tonse ndi a Yehova
Ndifedi banja limodzi
Kwanu kutalike bwanji,
Ndifedi
Banja limodzi.
Ndife mitundu yonse—
Ndifedi banja limodzi.
Timakondana kwambiri
Tilitu m’banja la Yehova!
Fiji, Tahiti, ndi New Caledonia;
Navajo, Blackfoot, ndi Cherokee;
Azerbaijan, Kazakhstan, ndi Estonia—
Ndifedi banja limodzi.