Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Makolo Anga Azindikhulupirira?

Kodi Ndingatani Kuti Makolo Anga Azindikhulupirira?

 Zimene muyenera kudziwa

 Makolo anu amayamba kukukhulupirirani potengera mmene mumachitira zinthu. Kumvera malamulo a makolo kuli ngati kubweza ngongole kubanki. Mukabweza ngongoleyo mokhulupirika, a banki angakudalireni n’kukupatsaninso mwayi wobwereka ngongole yaikulu. N’chimodzimodzinso ndi makolo. Mukamawamvera amayamba kukupatsaninso ufulu wambiri. Koma ngati nthawi inayake munkachita zinthu mosakhulupirika, sangakupatseni ufulu wonse umene mumafuna.

 Pamatenga nthawi kuti ayambe kukukhulupirirani. Makolo anu amafuna aone kuti ndinu munthu wodalirika, asanakupatseni ufulu wambiri.

 NKHANI IMENE INACHITIKADI: Craig ananena kuti: “Ndinkadziwa ndithu zimene makolo anga ankafuna kuti ndizichita. Koma m’malo mochita zimenezo, ndinkangokhala ngati ndikuchita zomwe akufunazo kwinaku n’kumachita zanga mwachibisira. Zimenezi zinkachititsa kuti asamandikhulupirire. Kenako ndinaona kuti ndikudzinamiza ndekha moti ndinaphunzira kuti, ‘ngati ndikufuna kuti makolo anga azindikhulupirira, ndiyambe ndine kukhala wokhulupirika.’”

 Zimene mungachite

 Muzinena zoona ngakhale zitakhala zovuta. Tonse timalakwitsa nthawi zina. Koma kulankhula zabodza kapena kubisa chilungamo pa nkhani inayake, kungachititse kuti makolo anu asiyiretu kukukhulupirirani. Ngati mutayesetsa kumachita zinthu moona mtima n’kumavomereza zomwe mwalakwitsa, makolo anu sangamakukaikireni. Aliyense akamachita zimenezi m’pamene anthu amayamba kumudalira.

 Anna ananena kuti: “Si kuti nthawi zonse anthu angasiye kukukhulupirirani chifukwa choti mumalakwitsa zinthu. Koma akhoza kusiya kukukhulupirirani ngati nthawi zonse mumakhalira kubisa zomwe mwalakwitsazo.”

 Baibulo limati: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheberi 13:18.

  •   Zoti muganizire: Kodi mumanena chilungamo makolo anu akakufunsani komwe mukupita komanso zomwe mukukachita? Nanga akakufunsani za kumene munapita ndiponso zomwe mumachita, kodi mumabisa zina ndi zina zomwe makolo anuwo akanafuna kudziwa?

 Muzisonyeza kuti ndinu wodalirika. Muzimvera malamulo onse omwe makolo angakupatseni. Muzigwira ntchito zapakhomo pa nthawi yake. Muzichita zinthu pa nthawi yomwe mwagwirizana. Musamalephere kulemba homuweki kapena kuwerenga za kusukulu. Muzionetsetsa kuti mwafika pakhomo pa nthawi yomwe makolo anakuuzani.

 Mnyamata wina dzina lake Ryan ananena kuti: “Ngati makolo akulola kuti ukasangalaleko ndi anzako, n’kukuuza kuti pofika 9 koloko usiku ukhale utafika, iwe n’kupezeka kuti wabwera cha m’ma 10, ungodziwiratu kuti zako zada. Sadzakulolanso kuti ukacheze ndi anzako.”

 Baibulo limati: “Pakuti aliyense ayenera kunyamula katundu wake.”​—Agalatiya 6:5.

  •   Zoti muganizire: Kodi makolo anu amaona kuti ndinu munthu wotani, kodi amaona kuti mumafika pakhomo pa nthawi yake, kugwira ntchito zapakhomo ndiponso kumvera malamulo omwe anakuikirani, ngakhale ataoneka kuti sakusangalatsani?

 Muzileza mtima. Ngati makolo anu atasiya kukukhulupirirani chifukwa cha zomwe munachita, dziwani kuti zingatenge nthawi kuti ayambirenso kukukhulupirirani. Chofunika n’kuleza mtima basi.

 Rachel ananena kuti: “Nditafika msinkhu winawake, ndinakhumudwa kuona kuti makolo anga sankandipatsabe ufulu wochita zinthu zina. Sindinkadziwa kuti kukhala ndi zaka zambiri n’kosiyana ndi kuchita zinthu ngati wamkulu. Ndinapempha makolo anga kuti andipatse mwayi woti ndiwasonyeze kuti ndine munthu wodalirika. Zinatenga nthawi komabe pamapeto pake zinatheka. Ndinaphunzirapo kuti msinkhu pawokha si umene umachititsa kuti makolo ayambe kukukhulupirira, koma zochita zako.”

 Baibulo limati: “Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.”—2 Akorinto 13:5.

  •   Zoti muganizire: Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe mungachite ngati mukufuna kuti makolo anu azikukhulupirirani kapena kuyambiranso kukukhulupirirani?

 ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI: Dziikireni zolinga kaya pa nkhani yochita zinthu pa nthawi yake, kugwira ntchito zapakhomo, kufika panyumba nthawi yabwino kapenanso pa zinthu zina. Fotokozerani makolo anu zomwe mwakonzazo komanso apempheni kuti akuuzeni zomwe angakonde kuti muzichita kuti azikukhulupirirani. Kenako chitani khama potsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Muvule umunthu wakale umene umagwirizana ndi khalidwe lanu lakale.” (Aefeso 4:22) Pakapita nthawi makolo anu adzaona okha kuti mwasintha.