Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?—Gawo 3

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?—Gawo 3

Nthawi zambiri achinyamata amakhala amphamvu ndipo sadwaladwala. Komabe pali ena amene ali ndi matenda aakulu. Kodi inunso mukudwala matenda aakulu? Ngati zili choncho, zitsanzo za V’loria, Justin ndi Nisa, omwe ndi a Mboni za Yehova, zingakulimbikitseni kwambiri. Onani zimene zimawathandiza kupirira matenda awo.

  • V’loria

  • Justin

  • Nisa

V’loria

Ndili ndi zaka 14, ndinayamba kudwala matenda omwe amachititsa thupi kuphwanya kwambiri. Pamene ndinkafika zaka 20, ndinapezekanso ndi nyamakazi, matenda omwe amachititsa thupi kutupa komanso ena omwe amafalitsidwa ndi utitiri. Popeza thupi langa linkakhala lofooka, zinkandivuta kuchita zonse zimene ndinkafuna. Nthawi zina, miyendo yanga inkasiya kugwira ntchito moti ndinkafunika kuyendera njinga ya olumala.

Koma vuto lalikulu linali lakuti ndinkavutika maganizo kwambiri chifukwa sindinkatha kuchita zinthu zing’onozing’ono monga kulemba kapena kutsegula botolo. Ndikaona ana akuyenda, ndinkadandaula chifukwa sindinkatha kuyenda bwinobwino ngati anawo. Ndinkadziona kuti ndine wolephera.

Ndikuthokoza kwambiri kuti achibale anga ndiponso ena mumpingo wa Mboni za Yehova ankandithandiza kwambiri. Anthu a mumpingo ankakonda kubwera kudzandiona ndipo izi zinkathandiza kuti ndisamasowe wocheza naye. Ena ankandiitana kuti ndikacheze nawo. Ankachita zimenezi ngakhale kuti zinali zovuta kuti andichotse panjinga yomwe ndinkayendera n’kundithandiza kukwera galimoto, kenako n’kunditsitsanso.

Abale ndi alongo achikulire mumpingo wathu ankandithandiza kwambiri chifukwa ankadziwa mmene munthu amamvera akamadwaladwala. Ankandilimbikitsa kuti ndisamaganizire kwambiri za mavuto anga kapena kudandaula kuti sindingachite zimene anthu ena amachita. Ndimakhala wosangalala kwambiri ndikakhala kumisonkhano kapena mu utumiki. (Aheberi 10:25) Ndikamachita zimenezi ndimazindikira kuti ndine wofanana ndi aliyense ngakhale kuti ndili ndi matenda aakulu.

Ndimadziwa kuti nthawi zonse Yehova amatithandiza kuti tithe kupirira mavuto athu. Baibulo limanena kuti ngakhale thupi la munthu litafooka kwambiri, munthu wamkati ‘amakhala watsopano tsiku ndi tsiku.’ (2 Akorinto 4:16) Umu ndi mmene ndimamvera.

Zoti muganizire: Ngati muli ndi matenda aakulu, kodi n’chifukwa chiyani muyenera kulola anthu ena kuti azikuthandizani? Ngati ndinu wathanzi, kodi mungathandize bwanji munthu amene akudwala?—Miyambo 17:17.

Justin

Tsiku lina ndinagwa pansi n’kukanika kudzukanso. Pamtima panangomangika ndipo ndinkalephera kuchita chilichonse. Kenako ananditengera kuchipatala. Poyamba madokotala sanandipeze ndi vuto lililonse. Koma kenako anapeza kuti ndili ndi matenda enaake amene amafalitsidwa ndi utitiri.

Matendawa anasokoneza kwambiri thupi langa. Ngakhale kuti tsopano padutsa zaka zambiri kuchokera pamene anandipeza ndi matendawa, nthawi zina manja anga amangonjenjemera okha. Masiku ena thupi langa lonse limaphwanya ndipo pena, zala zanga zimapweteka moti sinditha kuzisuntha. Zimakhala ngati molumikizira mafupamu mwachita dzimbiri ndipo sinditha kuchita chilichonse.

Ndinkadziona kuti ndidakali wamng’ono ndipo sindiyenera kumadwaladwala chonchi. Izi zinkandichititsa kukhala wosasangalala. Ndinkalira tsiku lililonse n’kumafunsa Mulungu kuti, “N’chifukwa chiyani mukulola kuti ndizivutika?” Ndinayamba kuganiza kuti Mulungu wandiiwala. Koma kenako ndinaganizira nkhani ya m’Baibulo yokhudza Yobu. Iye sanadziwe chifukwa chake ankakumana ndi mavuto, koma anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu. Ndinkaona kuti ngati Yobu anakwanitsa kukhala wokhulupirika, inenso ndikhoza kuchita zimenezi.

Akulu a mumpingo wathu amandithandiza kwambiri. Nthawi zonse amandifunsa mmene ndikumvera. Tsiku lina mkulu wina anandiuza kuti ndizimuimbira foni nthawi ina iliyonse imene ndikufuna kulankhula naye. Ndimathokoza Yehova tsiku lililonse chifukwa chondipatsa anzanga ngati amenewa.—Yesaya 32:1, 2.

Nthawi zina tikamadwala matenda aakulu timaiwala kuti Yehova amadziwa zonse zimene tikupirira. Paja Baibulo limati: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.” (Salimo 55:22) Ndimayesetsa kuchita zimenezi tsiku lililonse.

Zoti muganizire: Kodi anthu ena angakuthandizeni bwanji kuti muzipirira matenda anu?—Miyambo 24:10; 1 Atesalonika 5:11.

Nisa

Ndili ndi zaka pafupifupi 15, anandipeza ndi matenda ofooketsa thupi. Matendawa amatha kuwononga mtima, maso komanso ziwalo zina za thupi. Sikuti ndimamva kupweteka tsiku lililonse komabe nthawi zina ndimamva ululu waukulu zedi.

Atangondipeza ndi matendawa, ndinkangokhalira kulira. Ndinkaona kuti ndisiya kuchita zinthu zina zomwe ndinkazikonda. Mwachitsanzo, munthune ndimakonda kwambiri kuvina. Koma ndinkada nkhawa ndikaganizira kuti mwina sindidzathanso kuchita zimenezi, ngakhalenso kuyenda kumene.

Mkulu wanga ankandilimbikitsa kwambiri. Ankandithandiza kuti ndisamadzimvere chisoni chifukwa cha matenda angawa. Anandiuza kuti ndikamaopa chilichonse sindingathe kukhala ndi moyo wosangalala. Ankandilimbikitsanso kuti ndizipempha Yehova kuti andithandize chifukwa ndi amene amadziwa mmene ndikumvera.​—1 Petulo 5:7.

Lemba limene limandilimbikitsa kwambiri ndi la Salimo 18:6 lomwe limati: “Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova. Ndinafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake. Pamenepo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.” Lembali linandithandiza kudziwa kuti ndikapemphera kwa Yehova iye adzamva ndipo adzandilimbikitsa. Iye ndi wokonzeka kundithandiza nthawi zonse.

Ndazindikira kuti si kulakwa kudandaula tikakumana ndi mavuto chifukwa ndi zimene tonse timachita mwachibadwa. Koma sitiyenera kumangokhalira kudandaula chifukwa izi zingasokoneze moyo wathu komanso ubwenzi wathu ndi Mulungu. Tizikumbukira kuti Yehova si amene amachititsa mavuto athu. Koma nthawi zonse amatithandiza tikamaona kuti kumutumikira ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu.​—Yakobo 4:8.

Zoti muganizire: Kodi Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika?​—Yakobo 1:13.