Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Ndingatani Ngati Ndaboweka?

Ndingatani Ngati Ndaboweka?

 Mvula ikayamba kugwa masana, achinyamata ena amaboweka chifukwa amangokhala pakhomo popanda zochita komanso amasowa kolowera. Mnyamata wina dzina lake Robert ananena kuti: “Zikatere, chilichonse chimaima ndipo ndimasowa chochita.”

 Ngati nanunso munamvapo choncho, nkhaniyi ingakuthandizeni.

 Zimene muyenera kudziwa

  •   Kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono sikungakuthandizeni.

     Kugwiritsa ntchito intaneti kukhoza kuoneka ngati njira yotaitsirako nthawi. Komabe ikhoza kukuchititsani kuti muzilephera kuganizira zinthu zofunika. Ndipo zikatero m’pamene mumaona kuti palibe chomwe chikukuyenderani. Mnyamata wina dzina lake Jeremy wazaka 21 ananena kuti: “Ukhoza kukhala pansi n’kumaonerera sikirini koma osaonapo chilichonse chifukwa maganizo amakhala ali kwina.”

     Mtsikana wina dzina lake Elena ananenanso kuti: “Zipangizo zamakono sizingakupatse chilichonse chomwe ungafune. Zimangokupomboneza kuti usaganizire kwenikweni mmene zinthu zilili. Moti ukasiya kuzigwiritsa ntchito m’pamene umabowekanso kwambiri.”

  •   Zimadalira mmene mukuonera zinthu.

     Kodi ukakhala ndi zochita zambiri m’pamene ukhoza kumva kuti zikukuyendera? Zimangodalira ngati ukuikirapo mtima pa zomwe ukuchitazo. Mwachitsanzo mtsikana wina dzina lake Karen ananena kuti: “Sukulu inkandibowa ngakhale kuti nthawi zonse ndinkakhala ndi zambiri zoti ndichite. Umangofunika kuikirapo mtima kwambiri pa zomwe ukuchitazo. Ukatero m’pamene umasangalala.”

 Kodi mukudziwa? M’malo mongokhala chifukwa chosowa zochita, muziona kuti nthawi iliyonse yomwe mungakhale nayo ili ngati dothi lachonde ndipo ingakupatseni mwayi wophunzira ndi kuwonjezera luso linalake.

Nthawi iliyonse yomwe mungakhale nayo ili ngati dothi lachonde, ingakupatseni mwayi wophunzira komanso kuwonjezera luso linalake

 Zimene mungachite

 Muziphunzira zinthu zina komanso kudziwana ndi anthu ena. Pezani anzanu atsopano. Phunzirani masewero, luso kapena kantchito kenakake. Pezani nthawi yofufuza nkhani ina yake. Anthu amene amachita chidwi ndi zinthu zosiyanasiyana, sasoweratu pogwira ngakhale atakhala okha komanso amakhala osangalatsa kucheza nawo.

 Lemba lothandiza: “Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse.”—Mlaliki 9:10.

 Melinda ananena kuti: “Chaposachedwa ndinayamba kuphunzira Chitchainizi cha Chimandalini. Ndinkachiphunzira tsiku lililonse. Nditayamba kuchiphunzira ndinayamba kuchikonda moti ndinayamba kuona kuti ndinkatsalira nthawi yonseyi. Ndimamva bwino ndikakhala ndi zochita zinazake. Ndimaona kuti zimandithandiza kuti bongo wanga usamagone komanso kugwiritsa ntchito mwanzeru nthawi yanga.”

 Muziganizira kwambiri cholinga chanu. Mukamaganizira cholinga chomwe mukupangira zinazake, simungagwe ulesi ndi zomwe mukuchitazo. Komanso mukamaganizira zomwe mukufuna kukwaniritsa, simungaone zochita za kusukulu ngati chimtolo.

 Lemba lothandiza: “Kwa munthu, palibe chabwino kuposa . . . kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.”—Mlaliki 2:24.

 Hannah ananena kuti: “Nditatsala pang’ono kumaliza sukulu, ndinkawerenga kwa maola 8 patsiku. M’mbuyomo sindinkakonda kuwerenga choncho ndinkafuna kukokera. Koma chifukwa ndinali ndi cholinga choti ndimalize maphunziro anga, zinandilimbikitsa kuti ndisagwe ulesi.”

 Muzivomereza kuti zinthu zina simungathe kuzisintha. Ngakhale chinthu chomwe mumafunitsitsa mutakhala nacho, chikhoza kukhala ndi zinthu zina zomwe simungazikonde. Komanso ngakhale anzanu omwe mumawakonda kwambiri, akhoza kusintha zinthu zomwe munagwirizana ndipo mukhoza kupezeka kuti mulibe zoti muchite nthawiyo ikafika. M’malo mokhumudwa ndi zomwe zachitikazo, muyenera kuvomereza kuti ndi mmene zimakhalira nthawi zina.

 Lemba lothandiza: “Munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.”—Miyambo 15:15.

 Ivy ananena kuti: “Mnzanga wina anandiuza kuti ndiziyesetsa kukhala wosangalala ngakhale pomwe ndili ndekhandekha. Anandiuza kuti zimafuna luso lapadera kuti nthawi zina uzitha kuchita zinthu ndi anthu ena komanso kuchita zinthu pawekha. Moti ndi zimene aliyense amafunika kuchita.”