Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Ndingatani Kuti Ndimalize Homuweki Yanga?

Ndingatani Kuti Ndimalize Homuweki Yanga?

“Zimanditopetsa kudzuka 1 koloko m’mawa kuti ndilembe homuweki. Zomwe umangoganiza ndi zoti ugone basi.”David.

“Nthawi zina ndinkawerenga mpaka cha m’ma hafu 4 m’mawa kenako n’kudzuka 6 koloko kuti ndizipita kusukulu. Zinkandisowetsa mtendere.”—Theresa.

Kodi mumapanikizika ndi Homuweki? Ngati ndi choncho nkhaniyi ikuthandizani kudziwa zoyenera kuchita.

 N’chifukwa chiyani aphunzitsi amakupatsani homuweki?

Pali zambiri, koma zina mwa zifukwazo ndi zoti homuweki . . .

  • imakuthandizani kukulitsa luso lodziwa zinthu

  • imakuthandizani kukhala odalirika

  • imakuthandizani kugawa bwino nthawi kuti muziigwiritsa ntchito mwanzeru

  • imakuthandizani kuti muzitha kugwiritsa ntchito zomwe akuphunzitsani a

“Aphunzitsi akapereka homuweki kwa ana, amafuna kuti akayeserere zomwe aphunzirazo, m’malo moti zizingolowera khutu lina n’kutulukira khutu linalo.”—Marie.

Masamu komanso phunziro la sayansi zimakuthandizani kuti muziganiza n’cholinga choti muzithana ndi mavuto mosavuta. Ndipo akatswiri amanena kuti zimenezi zimathandiza kupanga komanso kulimbitsa timitsempha tatsopano ta mu ubongo. Choncho homuweki ili ngati masewera olimbitsa ubongo wanu.

Kaya mumaona ubwino wa homuweki kapena ayi, zoona zake n’zakuti simungaithawe. Koma chosangalatsa n’chakuti, ngakhale kuti simungathe kuchepetsa homuweki yomwe mumapatsidwa kusukulu, mukhoza kuchepetsa nthawi yomwe mumalembera homuwekiyo. Tiyeni tione mmene mungachitire zimenezi.

 Zomwe zingakuthandizeni

Ngati mukulephera kumaliza homuweki yanu, sikuti mukufunika kuchita kudzipanikiza koma mukungofunika kumachita zinthu mwadongosolo. Tayeserani izi.

  • Choyamba: Muzidziwiratu zoyenera kuchita. Baibulo limanena kuti: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.” (Miyambo 21:5) Musanayambe kulemba homuweki, muziikiratu pabwino zinthu zonse zomwe muzigwiritse ntchito, n’cholinga choti musamayendeyende.

    Komanso muzisankha malo abwino oti musasokonezedwe. Ena amaona kuti ndi bwino kukhala kuchipinda komwe ndi kopanda phokoso. Pamene ena amaona kuti ndi bwino kupita kumalo ena monga kulaibulale.

    “Ukakhala ndi ndandanda yabwino yochitira zinthu zakusukulu imakuthandiza kuti uzigwiritsa ntchito nthawi mwanzeru. Ndipo ukadziwiratu zomwe ukuyenera kuchita komanso nthawi yake, umakhala opanda nkhawa.”—Richard.

  • Chachiwiri: Muzichita zinthu mwadongosolo. Baibulo limanena kuti: “Zinthu zonse zizichitika . . . mwadongosolo.” (1 Akorinto 14:40) Choncho muzikhala ndi ndandanda ya mmene mugwirire ntchito zomwe mwapatsidwa.

    Ena amayamba ndi kulemba ntchito zovuta. Pamene ena amayambira zophweka kuti akazimaliza asagwe ulesi kulemba ntchito zinazo. Ndiye muzisankha njira imene mukuona kuti ndi yabwino kwa inuyo.

    “Zimayenda bwino ukakhala ndi ndandanda moti umadziwiratu zimene ukuyenera kuchita ndipo umazichita mwadongosolo. Ukatero sumapanikizika ndi kulemba homuweki.”—Heidi.

  • Chachitatu: Yambanipo. Baibulo limanena kuti: “Musakhale aulesi pa ntchito yanu.” (Aroma 12:11) Choncho musamalole kuti zinthu zina zizikuwonongerani nthawi yomwe mukuyenera kulemba homuweki.

    Anthu ozengereza zinthu samaliza ntchito pa nthawi yake komanso amaigwira mothamanga kwambiri ndipo zotsatira zake sizikhala zabwino. Ndiye kuti muchepetseko nkhawa, mukangopatsidwa homuweki, muziyamba kuilemba mwamsanga.

    “Ndikangolandira homuweki n’kuyamba kuilemba nthawi yomweyo kapena ndikangoweruka kusukulu, sindikhala ndi nkhawa kuti homuwekiyo isokoneza zochita zina.”—Serina.

    YESANI IZI: Tsiku lililonse muzilemba homuweki yanu pa nthawi yofananayo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mukhale odziletsa komanso kuti musamasinthesinthe nthawi yochitira zinthu zakusukulu.

  • Cha nambala 4: Maganizo anu azikhala pa chinthu chimodzi. Baibulo limanena kuti: “Maso ako owala aziyang’anitsitsa patsogolo pako.” (Miyambo 4:25) Kuti mutsatire malangizowa, muyenera kupewa zinthu zomwe zingakusokonezeni mukamawerenga, makamaka zipangizo zamakono.

    Kufufuza zinthu pa intaneti komanso kutumizirana mameseji kumangowonjezera nthawi yoti mumalize kulemba homuweki. Koma maganizo anu akakhala pa chinthu chimodzi, simungamapanikizike komanso mukhoza kumakhala ndi nthawi yambiri yopuma.

    “N’zosavuta kusokonezeka ndi mafoni am’manja, makompyuta, magemu, komanso TV. Ndiyeno ndikamalemba homuweki ndimazimitsa foni komanso zinthu zina zomwe zingandisokoneze.”—Joel.

  • Cha nambala 5: Muzikhala ndi malire. Baibulo limanena kuti: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” (Afilipi 4:5) Choncho mukatopa ndi homuweki ndi bwino kuti muzipumula kaye, mwina mungachite zinthu monga kukayenda, kukwera njinga kapena kukathamanga.

    Koma ngati mukuona kuti mumapanikizika kwambiri ndi homuweki mungachite bwino kukambirana ndi aphunzitsi anu. Aphunzitsiwo akaona kuti mumayesetsa kuchita zonse zomwe mungathe, akhoza kukusinthirani zina ndi zina.

    “Si bwino kuti muzipanikizika komanso kukhumudwa chifukwa cha homuweki. Muzingochita zomwe mungakwanitse. Ndipotu homuweki ndi chimodzi mwa zinthu zomwe siziyenera kukudetsani nkhawa.”—Julia.

Dzifunseni kuti:

  • Kodi ndi zinthu ziti zomwe ndingafunikire ndikamalemba homuweki?

  • Kodi ndi nthawi iti yomwe ingakhale yabwino kulemba homuweki?

  • Kodi ndi malo ati omwe angakhale abwino?

  • Ndingatani kuti ndisamachite zinthu mozengereza?

  • Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingandisokoneze?

  • Ndingatani kuti zipangizo zamakono kapena zinthu zina zisamandisokoneze?

  • Kodi ndingatani kuti ndisamapanikizike ndi homuweki?

MFUNDO YOTI MUZIIKUMBUKIRA: Muzimvetsa zimene mukuyenera kuchita mukapatsidwa homuweki ndipo ngati muli ndi mafunso, muzifunsa aphunzitsi anu musanatuluke m’kalasi.

a Mfundozi zachokera m’buku la School Power, lolembedwa ndi Jeanne Schumm.