Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Maganizo Anga Azikhala pa Zimene Ndikupanga?

Kodi Ndingatani Kuti Maganizo Anga Azikhala pa Zimene Ndikupanga?

 N’chifukwa chiyani maganizo anga sakhala pa chinthu chimodzi?

“Panopa sindiwerenganso mabuku ngati mmene ndinkachitira kale. Sindifunanso kuwerenga ndime zitalizitali.”—Elaine.

“Ndimathamangitsa filimu ndikamaona kuti ikuchedwa kutha.”—Miranda.

“Foni yanga ikazima ndikupanga zinthu zinazake zofunikira ndimangokhalira kuganizira kuti, ‘Mwinatu wina wandilembera meseji?’”—Jane.

Kodi zipangizo zamakono zikuchititsa kuti anthu azivutika kuika maganizo pa chinthu chimodzi? Ena amanena kuti inde. Nicholas Carr, yemwe amalemba mabuku komanso kuthandiza mabungwe kudziwa zimene angachite kuti ntchito zawo ziziyenda bwino, analemba kuti: “Tikamagwiritsa ntchito kwambiri intaneti, timakhala tikuphunzitsa ubongo wathu kuti usamachedwe kusokonezeka, moti umayamba kuchita zinthu mofulumira kwambiri koma popanda kuganizirapo kwambiri.” a

Onani njira zitatu zimene zipangizo zamakono zingachititsire kuti maganizo athu asamakhale pa chinthu chimodzi.

  • Tikamalankhula. Mtsikana wina dzina lake Maria anati: “Nthawi zambiri ukamalankhula ndi munthu ngakhale pamasom’pamaso, maganizo ake akumakhala ali kwina. Akumapezeka kuti akulemba mameseji, kusewera magemu kapena kuona zimene zili pamalo ochezera a pa intaneti kwinaku akukumvetsera.”

  • Akakhala m’kalasi. Buku lina linati: “Ana ambiri asukulu amanena kuti amagwiritsa ntchito zipangizo zamakono ali m’kalasi mwina polemba mameseji, kuwerenga zinthu zosiyanasiyana pa intaneti kapena kuonera zosangalatsa,” ndipo zinthu zimenezi “sizikhala zogwirizana ndi maphunziro awo.”—Digital Kids.

  • Akamawerenga. Mnyamata wina wazaka 22 dzina lake Chris anati: “Chinthu chomwe chimandivuta kwambiri ndi kudziletsa kuti ndisayang’ane foni yanga ndikangoimva ikulira.” Ngati ndinu mwana wasukulu, kulola kuti zipangizo zanu zamakono zikusokonezeni kungachititse kuti muzitenga nthawi yaitali kwambiri mukulemba homuweki.

Mfundo yofunika: Zingamakuvuteni kuika maganizo anu pa chinthu chimodzi ngati mutalola kuti zipangizo zamakono zizikulamulirani komanso kukusokonezani.

Maganizo omwe sakhala pa chinthu chimodzi amakhala ngati hatchi yamisala. M’malo moti uziwalamulira, amakulamulira iweyo

 Kodi ndingatani kuti ndizikwanitsa kuika maganizo anga pa chinthu chimodzi?

  • Mukamalankhula ndi munthu. Baibulo limati: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.” (Afilipi 2:4) Mungasonyeze kuti mumaganizira ena mukamawamvetsera mwatcheru. Muziyang’ana munthu amene mukulankhula naye ndipo musamalole kuti zipangizo zamakono zikusokonezeni.

    “Mukamalankhula ndi munthu, muzidziletsa kuti musayang’ane foni yanu. Mungasonyezenso kuti mumalemekeza munthuyo mukamamumvetsera mwatcheru.”—Thomas.

    ZOMWE ZINGAKUTHANDIZENI: Mukamalankhula ndi munthu muziika foni yanu patali. Akatswiri amanena kuti foni ikakhala pafupi imachititsa kuti maganizo ako aziyendayenda chifukwa umakhala ngati ukuyembekezera kuti chinachake chichitika.

  • Mukakhala m’kalasi. Baibulo limanena kuti: “Muzimvetsera mwatcheru kwambiri.” (Luka 8:18) Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, ngati kusukulu kwanu amalola kugwiritsa ntchito intaneti muli m’kalasi, musamawerenge mameseji, kusewera magemu kapena kucheza ndi anzanu pa intaneti. M’malomwake, maganizo anu onse azikhala pa maphunziro.

    “Muzimvetsera mwatcheru mukakhala m’kalasi. Muzilemba notsi aphunzitsi akamaphunzitsa. Ngati ndi zotheka muzikhala kutsogolo kwa kalasi yanu kuti mupewe zinthu zosokoneza.”—Karen.

    ZOMWE ZINGAKUTHANDIZENI: Muzilemba notsi pamanja osati pakompyuta. Kafukufuku amasonyeza kuti kuchita zimenezi kumathandiza kuti munthu asamasokonezeke komanso amatha kukumbukira zimene waphunzira.

  • Mukamawerenga. Baibulo limati: “Upeze nzeru, upezenso luso lomvetsa zinthu.” (Miyambo 4:5) Zimenezi zimafuna kuganiza mozama m’malo mongowerenga zinthu mofulumira kuti ukhoze mayeso.

    “Ndikamawerenga, ndimatchera foni yanga kuti isandisokoneze ndipo maganizo anga onse amakhala pa zimene ndikuchita. Ndikamachita zimenezi ndimapewa kuwerenga mameseji. Ndiye m’mutu mwanga mukabwera chinachake chomwe sindikufuna kuchiiwala, ndimachilemba penapake.”—Chris.

    ZOMWE ZINGAKUTHANDIZENI: Mukamawerenga, muzikhala pamalo omwe palibe zomwe zingakusokonezeni. Malowo azikhala aukhondo komanso pasamakhale poti zinthu zangoti mbwee.

a Zachokera m’buku la mutu wakuti The Shallows—What the Internet Is Doing to Our Brains.