Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Kusewera Magemu a Pazipangizo Zamakono?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Kusewera Magemu a Pazipangizo Zamakono?

 Mafunso okhudza magemuwa

 M’dziko la United States, makampani opanga magemu a pazipangizo zamakono amapanga ndalama mabiliyoni ambirimbiri . . .

  1.   Kodi anthu ambiri amene amakonda kusewera magemuwa amakhala ndi zaka zingati?

    1.   18

    2.   30

  2.   Pa avereji, kodi anthu amene amakonda kusewera magemuwa ndi amuna kapena akazi?

    1.   Anthu 55 pa 100 alionse amakhala amuna ndipo anthu 45 otsalawo amakhala akazi

    2.   Anthu 15 pa 100 alionse amakhala amuna ndipo anthu 85 otsalawo amakhala akazi

  3.   Pa magulu awiri a anthuwa, kodi ndi gulu liti limene lili ndi anthu ochuluka zedi pa anthu onse amene amakonda kusewera magemuwa?

    1.   Akazi oyambira zaka 18

    2.   Amuna a zaka zosaposa 17

 Mayankho (achokera pa kafukufuku amene anachitika mu 2013):

  1.   B. 30.

  2.   A. Anthu 45 pa 100 alionse ndi akazi. Chiwerengerochi chinangotsala pang’ono kufika pa hafu ya anthu onse amene amakonda kusewera magemuwa.

  3.   A. Anthu 31 pa 100 alionse ndi akazi oyambira zaka 18, ndipo anthu 19 pa 100 alionse ndi amuna a zaka zosaposa 17.

 Zotsatira za kafukufuku ameneyu zingakuthandizeni kudziwa anthu amene amakonda kusewera magemu pazipangizo zamakono. Koma sizingakuthandizeni kudziwa mmene magemuwo amakhudzira anthu amene amawasewera.

 Ubwino wake

 Kodi mungagwirizane ndi mawu ati pa zimene anzanu ananena zokhudza kusewera magemu pazipangizo zamakono?

  •  “Kusewera magemu ndi abale ako komanso anzako kumathandiza kuti muzigwirizana kwambiri.”​—Irene.

  •  “Magemu amakuthandiza kuiwalako mavuto.”​—Annette.

  •  “Munthu amene amasewera magemu amakhala woganiza mwachangu.”​—Christopher.

  •  “Kusewera magemu kumathandiza munthu kukhala wanzeru.”​—Amy.

  •  “Ukamasewera magemu umakhala woganiza kwambiri. Umatha kuona bwinobwino mmene zinthu zilili, kupanga mapulani komanso kudziwa mmene ungachitire zinthu.”​—Anthony.

  •  “Magemu ena sungasewere wekha. Izi zimathandiza kuti uzitha kucheza komanso kuchita zinthu ndi ena.”​—Thomas.

  •  “Pamafunika mphamvu ndithu kuti usewere magemu ena. Magemu oterewa amathandiza kulimbitsa thupi.”​—Jael.

 Kodi mukugwirizana ndi mawu ena, kapenanso mawu onse amene anzanu ananenawa? N’zoona kuti magemu ena osewera pazipangizo zamakono angathandize kuti munthu aziganiza mofulumira kapenanso kuti akhale wamphamvu. Nthawi zina munthu amene wasowa chochita angataitseko nthawi posewera magemuwa, komanso mogwirizana ndi zimene Annette ananena, munthu amene akusewera magemuwo “angathe kuiwalako mavuto.” Ndipo zimenezi sikuti nthawi zonse zingakhale zolakwika.

 ● Baibulo limati “chilichonse chochitika padziko lapansi chilidi ndi nthawi yake.” Izi zikusonyeza kuti munthu ayenera kupeza nthawi yosangalala.—Mlaliki 3:1-4.

 Kuipa kwake

 Kodi mukuwononga nthawi yambiri posewera magemuwa?

 “Ndikangoyamba kusewera magemu, zimandivuta kwambiri kuti ndisiye. Mumtima mwanga ndimadziuza kuti, ‘Ndingosewera imodzi yokha.’ Koma ndimadzidzimuka ndikaona kuti ma awazi ambiri adutsa ndikusewera gemuyo.”​—Annette.

 “Kusewera magemu kungakuwonongetseni nthawi yambiri. Mukhoza kusewera magemuwa kwa ma awazi ambirimbiri n’kumaona kuti zinthu zikuyenda bwino chifukwa mwawina magemu 5 Koma zoona zake n’zakuti simupeza phindu lililonse ngakhale mutawina magemu ambirimbiri.”​—Serena.

 Mfundo yofunika kwambiri: Ngati mutawononga ndalama, mukhoza kupeza zina. Koma ngati mutawononga nthawi, singabwererenso. Choncho nthawi ndi chinthu chofunika kwambiri kuposa ndalama. Musalole kuti chilichonse chikuwonongetseni nthawi.

 ● Baibulo limati: “Pitirizani kuyenda mwanzeru . . . , ndipo muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”—Akolose 4:5.

 Kodi magemu a pazipangizo zamakono angakhudze mmene mumaganizira?

 “Munthu angathe kusewera gemu yosonyeza zinthu zoipa kwambiri, zomwe ngati atazichitadi osati pagemupo, munthuyo akhoza kumangidwa kapena kunyongedwa.”​—Seth.

 “Magemu ambiri anawakonza m’njira yakuti uzigonjetsa adani ako kuti uwine. Kawirikawiri posewera magemuwa umafunika kupha adaniwo mwankhanza kwambiri.”​—Annette.

 “Nthawi zina sungakhulupirire zimene ukulankhula kwa anzako amene akusewera nawo gemu. Umatha kukuwa kuti ‘Ifa iwe!’ kapena ‘Ndikuphatu!’”​—Nathan.

 Mfundo yofunika kwambiri: Muzipewa magemu amene amalimbikitsa zinthu zimene Mulungu amadana nazo, monga chiwawa, chiwerewere ndiponso kukhulupirira mizimu.​—Agalatiya 5:19-21; Aefeso 5:10; 1 Yohane 2:15, 16.

 ● Baibulo limati Yehova “amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa,” osati anthu okhawo ochita zachiwawa. (Salimo 11:5) Ngakhale kuti magemu amene mumakonda kusewera sangasonyeze khalidwe limene mungayambe kuchita m’tsogolomu, koma magemuwo amasonyeza khalidwe limene muli nalo panopa.

 Zoti muganizire: Buku linalake (Getting to Calm) linafotokoza kuti “ana amatengera kwambiri zimene amachita posewera magemu achiwawa poyerekezera ndi zimene amaona pa TV. Zili choncho chifukwa posewera magemuwa, samangoona munthu woopsa akupha anzake koma iwowo amakhala munthu woopsayo. Chifukwa choti munthu amaphunzira zinthu akamasewera magemu a pazipangizo zamakonowa, magemuwa ali ngati mphunzitsi wa zachiwawa.”​—Yerekezerani ndi Yesaya 2:4.

 Zimene zingakuthandizeni

 Achinyamata ambiri aphunzira kuchita zinthu mwanzeru pa nkhani yosewera magemu a pazipangizo zamakono. Taonani zitsanzo ziwirizi.

 “Ndinkakonda kusewera magemu mpaka pakati pa usiku. Ndinkaganiza kuti: ‘Aaa nthawi ilipo. Paja ine ndimafunikira kugona ma awazi 5 basi. Ndingosewera gemu inanso imodzi.’ Koma tsopano ndaphunzira kusewera magemuwa pa nthawi yoyenera. Ndimasangalala ndikamasewera magemuwa, koma ndaona kuti ndizisewera mwa apo ndi apo. Kudziletsa n’kofunika pochita chinthu chilichonse.”​—Joseph.

 “Panopa ndachepetsa kwambiri nthawi yosewera magemu. Zimenezi zandithandiza kuti ndizipeza nthawi yambiri yochita utumiki ndiponso yothandiza anthu ena mumpingo mwathu. Chinthu chinanso n’chakuti ndakwanitsa kupeza nthawi yophunzira piyano. Ndazindikira kuti pali zinthu zambiri zimene munthu ungachite, osati kumangosewera magemu basi.”​—David.

 ● Baibulo limanena kuti amuna ndi akazi oganiza bwino “sachita zinthu mopitirira malire.” (1 Timoteyo 3:2, 11) Anthu otere amapeza nthawi yosangalala koma amakhala ndi malire.​—Aefeso 5:10.

 Mfundo yofunika kwambiri: Kusewera magemu a pazipangizo zamakono angakhale osangalatsa ngati munthu akuwasewera pa nthawi yoyenera. Choncho musalole kuti magemuwo azikutherani nthawi kapena azikulepheretsani kuchita zinthu zina zofunika kwambiri pa moyo. M’malo moyesetsa kuti muwine posewera gemu, kodi simungachite bwino kuyesetsa kuti mukwanitse kuchita zinthu zofunika zimene mukufuna kuchita pa moyo wanu?